1 Mas. 51.14; Luk. 18.1 Yehova, Mulungu wa chipulumutso changa,
ndinafuula pamaso panu usana ndi usiku.
2Pemphero langa lidze pamaso panu;
munditcherere khutu kukuwa kwanga.
3Pakuti mzimu wanga wadzala nao mavuto,
ndi moyo wanga wayandikira kumanda.
4Anandiwerenga pamodzi nao otsikira kudzenje;
ndakhala ngati munthu wopanda mphamvu.
5Wotayika pakati pa akufa,
ngati ophedwa akugona m'manda,
amene simuwakumbukiranso;
ndipo anawadula kusiyana ndi dzanja lanu.
6Munandiika kunsi kwa dzenje,
kuli mdima, kozama.
7 Mas. 42.7 Mkwiyo wanu utsamira pa ine,
ndipo munandizunza ine ndi mafunde anu onse.
8Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali;
munandiika ndiwakhalire chonyansa.
Ananditsekereza, osakhoza kutuluka ine.
9 Yob. 11.13; Mas. 86.3 Diso langa lapuwala chifukwa cha kuzunzika kwanga:
Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse;
nditambalitsira manja anga kwa Inu.
10 Yes. 38.18 Kodi mudzachitira akufa zodabwitsa?
Kodi adzaukanso otisiyawo, ndi kukulemekezani?
11Adzafotokozera chifundo chanu kumanda kodi,
chikhulupiriko chanu kumalo a chionongeko?
12Zodabwitsa zanu zidzadziwika mumdima kodi,
ndi chilungamo chanu m'dziko la chiiwaliko?
13 Mas. 5.3; 119.147 Koma ndinafuulira kwa Inu, Yehova,
ndipo pemphero langa lifika kwa Inu mamawa.
14 Mas. 43.2; 13.1 Yehova mutayiranji moyo wanga?
Ndi kundibisira nkhope yanu?
15Wozunzika ine ndi wofuna kufa kuyambira ubwana wanga;
posenza zoopsa zanu, ndithedwa nzeru.
16Kuzaza kwanu kwandimiza;
zoopsa zanu zinandiononga.
17Zinandizungulira ngati madzi tsiku lonse;
zinandizinga pamodzi.
18Munandichotsera kutali wondikonda ndi bwenzi langa,
odziwana nane akhala kumdima.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.