LEVITIKO Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu
Mau OyambaBuku la Levitiko likukamba za malamulo a chipembedzo ndi miyambo yosiyanasiyana mu Israele wakale, komanso za malamulo okhudza ansembe amene anali ndi udindo woonetsetsa kuti malamulowo akutsatidwa bwino lomwe.Mutu waukulu mu bukuli ndiwakuti Yehova ndi Woyera ndipo anthu ake ayenera kukhala oyera mtima pa kupembedza kwao ndiponso moyo wao onse kuti ubale wao ndi Mulungu usasokonezeke.Mau amene amadziwika bwino kuchokera mu bukuli ndi omwe Yesu adawanena kuti ndilo lamulo lachiwiri lalikulu: “Udzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.” (19.18)Za mkatimuMalamulo onena za zopereka ndi nsembe 1.1—7.38Aroni ndi ana ake awadzoza kukhala ansembe 8.1—10.20Malamulo onena za mwambo wa kuyeretsedwa ndi kudetsedwa 11.1—15.33Za tsiku lotetezera 16.1-34Malamulo onena za chiyero pa moyo ndi pa chipembedzo 17.1—27.34