DEUTERONOMO Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu
Mau OyambaBukuli likutchedwa Deuteronomo, ndiye kuti “Kubwereza”, chifukwa likulongosola kachiwiri zina ndi zina zimene zidakambidwa kale m'mabuku ena aja. Bukuli likulongosola za malangizo osiyanasiyana amene Mose adapereka kwa ana a Israele pamene anali m'dziko la Mowabu, ali pafupi kulowa m'dziko lamalonjezano la Kanani.Phunziro lalikulu lopezeka m'bukuli ndi lakuti Yehova apulumutsa Aisraele ndi kuwadalitsa chifukwa amawakonda kwambiri. Motero iwonso ayenera kumakumbukira zimenezi ndi kumkonda Iyeyo potsata malamulo ake, kuti akhale ndi moyo ndi kulandirabe madalitso ena pa moyo wao ukudzawu. Mau odziwika kwambiri apezeka pa 6.4-6: “ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.” Paja Yesu adati, pa malamulo onse, lamulo lalikulu ndi lomweli.Za mkatimuMalangizo oyamba a Mose 1.1—4.49 Malangizo achiwiri a Mose 5.1—26.19a. Za Malamulo Khumi 5.1—10.22 b. Mose aperekanso malamulo ena ndi malangizo 11.1—26.19Machenjezo asanalowe m'dziko la malonjezano 27.1—28.68Yehova achita chipangano ndi anthu ake 29.1—30.20Malangizo otsiriza a Mose 31.1—34.12 a. Mose asankha Yoswa kuti adzalowe m'malo mwake 31.1—33.29 b. Imfa ya Mose 34.1-12