YESAYA 27 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Munda wampesa wa Yehova

1 Mas. 74.13-14 Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lake lolimba ndi lalikulu ndi lamphamvu adzalanga Leviyatani njoka yothamanga, ndi Leviyatani njoka yopindikapindika; nadzapha ching'ona chimene chili m'nyanja.

2 Yer. 2.21 Tsiku limenelo: munda wa mphesa wavinyo, imbani inu za uwo.

3Mas. 121.4-5Ine Yehova ndiusunga uwo; ndidzauthirira madzi nthawi zonse; ndidzausunga usiku ndi usana, kuti angauipse.

4Ndilibe ukali; ndani adzalimbanitsa lunguzi ndi minga ndi Ine kunkhondo? Ndiziponde ndizitenthe pamodzi.

5Yob. 22.21Kapena mlekeni, agwire mphamvu zanga, nachite nane mtendere; inde, achite nane mtendere.

6M'mibadwo ikudzayo Yakobo adzamera mizu; Israele adzaphuka ndi kuchita mphundu; ndipo iwo adzadzaza ndi zipatso padziko lonse lapansi.

7Kodi Mulungu wakantha Yakobo, monga umo anawakanthira akumkanthawo? Kapena kodi iye waphedwa malinga ndi kuphedwa kwa iwo amene anaphedwa ndi iye?

8Munalimbana naye pang'ono, pamene munamchotsa; wamchotsa iye kuomba kwake kolimba tsiku la mphepo yamlumbanyanja.

9Chifukwa chake, mwa ichi choipa cha Yakobo chidzafafanizidwa, ndipo ichi ndi chipatso chonse chakuchotsa tchimo lake; pamene iye adzayesa miyala yonse ya guwa la nsembe, ngati miyala yanjeresa yoswekasweka, zifanizo ndi mafano a dzuwa sizidzaukanso konse.

10Pakuti mzinda wotchingidwa uli pa wokha, mokhalamo mwa bwinja, ndi mosiyidwa ngati chipululu; mwanawang'ombe adzadya kumeneko, nadzagonako pansi, nadzamaliza nthambi zake.

11Yer. 8.7Ponyala nthambi zake zidzathyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; chifukwa chake Iye amene anawalenga sadzawachitira chisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.

12Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Yehova adzaomba tirigu wake, kuchokera madzi a nyanja, kufikira kumtsinje wa Ejipito, ndipo mudzakunkhidwa mmodzi, inu ana a Israele.

13 Mat. 24.31; Chiv. 11.15 Ndipo padzakhala tsiku limenelo, lipenga lalikulu lidzaombedwa; ndipo adzafika omwe akadatayika m'dziko la Asiriya, ndi opirikitsidwa a m'dziko la Ejipito; ndipo adzapembedza Yehova m'phiri lopatulika la pa Yerusalemu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help