1Ndipo mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena; likukhalireni inu tsiku lakuliza malipenga.
2Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya fungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe imodzi yamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi opanda chilema;
3ndi nsembe yao yaufa, ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombeyo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo,
4ndi limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo ndi anaankhosa asanu ndi awiri;
5ndi tonde mmodzi wa nsembe yauchimo, yakutetezera inu;
6pamodzi ndi nsembe yopsereza ya pamwezi, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, monga mwa lemba lake, zikhale za fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.
7 Mas. 35.13; Yes. 58.5 Ndipo tsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri uwu muzikhala nako kusonkhana kopatulika; pamenepo mudzichepetse, musamagwira ntchito;
8Num. 28.31koma mubwere nayo nsembe yopsereza kwa Yehova, ya fungo lokoma; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; akhale kwa inu opanda chilema;
9ndi nsembe yao ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodziyo;
10limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo ndi anaankhosa asanu ndi awiri;
11tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo, pamodzi ndi nsembe yauchimo yotetezera, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira.
12Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiwiri muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena, koma muchitire Yehova madyerero masiku asanu ndi awiri;
13ndipo mubwere nayo nsembe yopsereza, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe zamphongo khumi ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, akhale opanda chilema;
14ndi nsembe yake yaufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a efa wa ng'ombe imodzi, momwemo nazo ng'ombe khumi ndi zitatuzo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi, momwemo nazo nkhosa zamphongo ziwirizo;
15ndi limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo nao anaankhosa khumi ndi anai;
16ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.
17Ndipo tsiku lachiwiri muzibwera nazo ng'ombe zamphongo khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai a chaka chimodzi, opanda chilema;
18ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;
19ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira.
20Ndi tsiku lachitatu ng'ombe khumi ndi imodzi, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai a chaka chimodzi opanda chilema;
21ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;
22ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.
23Ndi tsiku lachinai ng'ombe khumi, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, opanda chilema;
24nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;
25ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.
26Ndi tsiku lachisanu ng'ombe zisanu ndi zinai, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, opanda chilema;
27ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;
28ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.
29Ndi tsiku lachisanu ndi chimodzi ng'ombe zisanu ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, opanda chilema;
30ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;
31ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.
32Ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri ng'ombe zisanu ndi ziwiri, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, opanda chilema;
33ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa yamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;
34ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.
35 Yoh. 7.37 Tsiku lachisanu ndi chitatu muzikhala nalo tsiku loletsa; musamachita ntchito ya masiku ena;
36koma mubwere nayo nsembe yopsereza ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri, a chaka chimodzi, opanda chilema;
37nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;
38ndi tonde mmodzi wa nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosakeleza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.
39 Lev. 23.2, 4 Izi muzikonzera Yehova mu zikondwerero zanu zoikika, pamodzi ndi zowinda zanu, ndi zopereka zanu zaufulu, za nsembe zanu zopsereza, ndi za nsembe zanu zaufa, ndi za nsembe zanu zothira, ndi za nsembe zanu zoyamika.
40Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.