YAKOBO Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu
Mau OyambaWolemba kalatayi alembera Akhristu achiyuda obalalika kumaiko osiyanasiyana. Apereka malangizo amitundumitundu owathandiza kuwongolera moyo wao wa masiku onse mwa njira ya Chikhristu. Aziwonetsa makhalidwe abwino pa zochita zao zonse, pakuti “chikhulupiriro, chikapanda kukhala nacho ntchito, chikhala chakufa m'kati mwakemo.” (2.17)Za mkatimuMau oyamba 1.1Za chikhulupiriro ndi nzeru 1.2-8Za umphawi ndi chuma 1.9-11Za kuyesedwa ndi zovuta kapena zinyengo 1.12-18Za kumva ndi kuchita zimene Mulungu anena 1.19-27Awachenjeza kuti asamachite tsankho 2.1-13Za chikhulupiriro ndi ntchito zake 2.14-26Za kuwongolera lilime potsata nzeru zochokera kumwamba 3.1-18Za kuchita chibwenzi ndi pansi pano 4.1—5.6Za kuyembekeza mopirira ndi kupempherera odwala 5.7-20