1Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chimodzi, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,
2Yes. 23; Amo. 1.9-10Wobadwa ndi munthu iwe, popeza Tiro ananyodola Yerusalemu, ndi kuti, Ha! Wathyoka uwu udali chipata cha mitundu ya anthu; wanditembenukira ine; ndidzakhuta ine, wapasuka uwu;
3chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndikutsutsa iwe, Tiro, ndidzakukweretsera amitundu, monga nyanja iutsa mafunde ake.
4Ndipo adzagumula malinga a Tiro, ndi kugwetsa nsanja zake; inde ndidzausesa fumbi lake, ndi kuuyesa pathanthwe poyera.
5Udzakhala poyanika khoka pakati pa nyanja, pakuti Ine ndachinena, ati Ambuye Yehova; ndipo udzakhala chofunkha cha amitundu.
6Ndi ana ake aakazi okhala kumunda adzaphedwa ndi lupanga; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
7Ezk. 29.18Pakuti atero Ambuye Yehova, Taona ndidzafikitsira Tiro Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mfumu ya mafumu, yochokera kumpoto ndi akavalo, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi msonkhano wa anthu ambiri.
8Ana ako aakazi adzawapha kumunda ndi lupanga; ndipo adzakumangira nsanja, ndi kukuundira mtumbira, ndi kukuimikira chikopa.
9Nadzaikira malinga ako zogumulira, nadzagwetsa nsanja zako ndi zida zake.
10Popeza achuluka akavalo ake, fumbi lao lidzakukuta; malinga ako adzagwedezeka ndi phokoso la apakavalo, ndi njinga za magaleta, polowa iye pa zipata zako, monga umo amalowera m'mzinda popasukira linga lake.
11Ndi ziboda za akavalo ake iye adzapondaponda m'makwalala ako onse; adzapha anthu ako ndi lupanga; ndi zoimiritsa za mphamvu yako zidzagwa pansi.
12Ndipo adzalanda chuma chako ndi kufunkha malonda ako, nadzagwetsa malinga ako ndi kupasula nyumba zako zofunika, nadzaponya miyala yako, ndi mitengo yako, ndi fumbi lako, m'madzi.
13Ndipo ndidzaleketsa phokoso la nyimbo zako, ndi kulira kwa mazeze ako sikudzamvekanso.
14Ndipo ndidzakuyesa pathanthwe poyera; udzakhala poyanika khoka, sadzakumanganso; pakuti Ine Yehova ndachinena, ati Ambuye Yehova.
15 Ezk. 27.28 Atero Ambuye Yehova kwa Tiro, Zisumbu sizidzagwedezeka nanga pomveka kugwa kwako, pobuula olasidwa, pakuchitika kuphako pakati pako?
16Yes. 23.8Pamenepo akalonga onse a kunyanja adzatsika ku mipando yachifumu yao, nadzavula zovala zao zopikapika, nadzavala kunjenjemera, nadzakhala panthaka pansi, nadzanjenjemera mphindi zonse ndi kudabwa nawe.
17Ezk. 27.32Ndipo adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kunena nawe, Watayika bwanji, ndiwe pokhala pa anthu a panyanja, mzinda womveka, unalimbika panyanja, uwo ndi okhalamo, amene anakhalitsa kuopsa kwao pa onse okhala momwemo!
18Pamenepo zisumbu zidzanjenjemera tsiku la kugwa kwako, inde zisumbu za kunyanja zidzatenga nkhawa pa kuchokera kwako.
19Ezk. 27.34Pakuti atero Ambuye Yehova, Pamene ndikusandutsa mzinda wopasuka, ngati mizinda yosakhalamo anthu, ndi kukukweretsera nyanja, nadzakumiza madzi aakulu;
20pamenepo ndidzakutsitsa nao otsikira kumanda, kwa anthu a kale lomwe, ndi kukukhalitsa kumalo a kunsi kwa dziko, kopasukira kale lomwe, pamodzi nao otsikira kumanda, kuti mwa iwe musakhale anthu; ndipo ndidzaika ulemerero m'dziko la amoyo,
21Ezk. 27.36ndidzakuika woopsa; ndipo sudzaonekanso, chinkana akufunafuna sudzapezekanso konse, ati Ambuye Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.