EKSODO 35 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Zopereka zofunika za pa chihemacho

1Ndipo Mose anasonkhanitsa khamu lonse la ana a Israele, nanena nao, Siwa mau amene Yehova analamula, kuti muwachite.

2Eks. 20.8Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri muliyese lopatulika, Sabata lakupuma la Yehova: aliyense agwira ntchito pamenepo, aphedwe.

3Musamasonkha moto m'nyumba zanu zilizonse tsiku la Sabata.

4Ndipo Mose ananena ndi khamu lonse la ana a Israele, ndi kuti, Ichi ndi chimene Yehova analamula ndi kuti,

5Eks. 25.2Mumtengere Yehova chopereka cha mwa zanu; aliyense wa mtima womfunitsa mwini abwere nacho, ndicho chopereka cha Yehova; golide, ndi siliva, ndi mkuwa;

6ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi;

7ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;

8ndi mafuta akuunikira, ndi zonunkhira za mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma;

9ndi miyala yasohamu, ndi miyala yoika ya efodi, ndi ya chapachifuwa.

Zipangizo za m'malo opatulika(Eks. 39.32-43)

10Ndipo abwere yense wa mtima waluso mwa inu, napange zonse zimene Yehova analamula;

11chihema, ndi chophimba chake, zokowera zake, ndi matabwa ake, mitanda yake, mizati, nsanamira, ndi nsichi zake, ndi makamwa ao;

12likasa, ndi mphiko zake, chotetezerapo, ndi nsalu yotchinga yotseka;

13gome, ndi mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, ndi mkate woonekera;

14ndi choikaponyali cha kuunika, ndi zipangizo zake, ndi nyali zake, ndi mafuta a kuunika;

15ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi mphiko zake, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsalu yotsekera pakhomo, pa khomo la chihema;

16guwa la nsembe yopsereza, ndi sefa wamkuwa, mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, mkhate ndi tsinde lake;

17nsalu zotchingira za kubwalo, nsichi zake, ndi makamwa ake, ndi nsalu yotsekera ku chipata cha pabwalo;

18zichiri za chihema, ndi zichiri za kubwalo, ndi zingwe zao;

19zovala za kutumikira nazo m'malo opatulika, zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, zakugwira nazo ntchito ya nsembe.

Anthu abwera ndi zopereka mwaufulu

20Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka pamaso pa Mose.

21Eks. 35.5Ndipo anadza, aliyense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wake wamfunitsa, nabwera nacho chopereka cha Yehova, cha ku ntchito ya chihema chokomanako, ndi ku utumiki wake wonse, ndi ku zovala zopatulika.

22Ndipo anadza amuna ndi akazi, onse akufuna mtima eni ake, nabwera nazo mphete za mphuno, mphete za m'makutu, ndi mphete zosindikizira, ndi zigwinjiri, zonsezi zokometsera za golide; inde yense wakupereka kwa Yehova chopereka chagolide.

23Ndipo aliyense kwao kunapezeka lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi, ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, anabwera nazo.

24Yense wakupereka chopereka cha siliva ndi mkuwa, anabwera nacho chopereka cha Yehova; ndi yense amene kwao kunapezeka mtengo wakasiya wa ku machitidwe onse a ntchitoyi, anabwera nao.

25Miy. 31.19, 22, 24Ndi akazi onse a mtima waluso anapota ndi manja ao, nabwera nalo thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

26Ndi akazi onse ofulumidwa mtima ndi luso anapota ubweyawo wa mbuzi.

27Ndi akulu anabwera nayo miyala yasohamu, ndi miyala yoti aiike kuefodi, ndi kuchapachifuwa;

28ndi zonunkhira, ndi mafuta akuunikira, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza za fungo lokoma.

29Amuna ndi akazi onse a ana a Israele amene mitima yao inawafunitsa eni kubwera nazo za ku ntchito yonse imene Yehova analamula ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera nacho chopereka chaufulu, kuchipereka kwa Yehova.

Za amisiri opanga ntchitoyi(Eks. 31.1-11)

30Ndipo Mose anati kwa ana a Israele, Taonani, Yehova anaitana, ndi kumtchula dzina lake, Bezalele, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda;

31ndipo anamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, za m'ntchito zilizonse;

32kulingirira ntchito zaluso, kuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa;

33ndi kuzokota miyala yoikika, ndi kuzokota mitengo, kuchita m'ntchito zilizonse zaluso.

34Ndipo anaika m'mtima mwake kuti alangize ena, iye ndi Oholiyabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani.

35Eks. 26.1-14Amenewo anawadzaza ndi luso lamtima, lakuchita ntchito zilizonse, ya kuzokota miyala, ndi ya mmisiri waluso, ndi ya wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ya muomba, ya iwo akuchita ntchito iliyonse, ndi ya iwo olingirira ntchito yaluso.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help