1 Yow. 1.20 Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje;
motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.
2 Mas. 63.1; Yoh. 7.37 Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu,
la kwa Mulungu wamoyo.
Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?
3 Mas. 79.10; 80.5 Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa,
usana ndi usiku;
pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse,
Mulungu wako ali kuti?
4 Mas. 62.8; Yes. 30.29 Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine,
pakuti ndinkapita ndi unyinji wa anthu,
ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu,
ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika,
ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.
5 Mas. 43.5 Udziweramiranji moyo wanga iwe?
Ndi kuzingwa m'kati mwanga?
Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso
chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.
6Mulungu wanga, moyo wanga
udziweramira m'kati mwanga;
chifukwa chake ndikumbukira Inu m'dziko la Yordani,
ndi mu Aheremoni, m'kaphiri ka Mizara.
7 Yon. 2.3 Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya,
pa mkokomo wa matiti anu;
mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine.
8 Mas. 77.6; Mac. 16.25 Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake,
ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine.
Inde pemphero la kwa Mulungu wa moyo wanga.
9 Mas. 43.2 Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa,
mwandiiwala chifukwa ninji?
Ndimayenderanji wakulira
chifukwa cha kundipsinja mdaniyo?
10 Mas. 42.3 Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga;
pakunena ndine dzuwa lonse,
Mulungu wako ali kuti?
11 Mas. 42.5 Udziweramiranji moyo wanga iwe?
Ndi kuzingwa m'kati mwanga?
Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso,
ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.