1 Eks. 14.24-25; Mas. 43.1 Tsutsanani nao iwo akutsutsana nane, Yehova;
limbanani nao iwo akulimbana nane.
2Gwirani chikopa chotchinjiriza,
ukani kundithandiza.
3Sololani nthungo, ndipo muwatsekerezere kunjira akundilondola.
Nenani ndi moyo wanga,
Chipulumutso chako ndine.
4 Mas. 40.14-15 Athe nzeru nachite manyazi iwo akufuna moyo wanga;
abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira chiwembu.
5 Mas. 1.4 Akhale monga mungu kumphepo,
ndipo mngelo wa Yehova awapirikitse.
6Njira yao ikhale ya mdima ndi yoterera,
ndipo mngelo wa Yehova awalondole.
7Pakuti ananditchera ukonde wao m'mbunamo kopanda chifukwa,
anakumbira moyo wanga dzenje kopanda chifukwa.
8 1Ate. 5.3 Chimgwere modzidzimutsa chionongeko;
ndipo ukonde wake umene anautcha umkole yekha mwini,
agwemo, naonongeke m'mwemo.
9 Mas. 13.5 Ndipo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova;
udzasekera mwa chipulumutso chake.
10 Eks. 15.11 Mafupa anga onse adzanena,
Yehova, afanana ndi Inu ndani,
wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu,
ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?
11 Mas. 27.12 Mboni za chiwawa ziuka,
zindifunsa zosadziwa ine.
12 Yoh. 10.32 Andibwezera choipa m'malo mwa chokoma,
inde, asaukitsa moyo wanga.
13Koma ine, pakudwala iwowa, chovala changa ndi chiguduli.
Ndinazunza moyo wanga ndi kusala;
ndipo pemphero langa linabwera kuchifuwa changa.
14Ndakhala ine monga ngati iye anali bwenzi langa,
kapena mbale wanga;
polira ndinaweramira pansi,
monga munthu wakulira maliro amai wake.
15Ndipo pakutsimphina ine anakondwera,
nasonkhana pamodzi;
akundipanda anandisonkhanira; ndipo sindinachidziwe,
ananding'amba osaleka.
16Pakati pa onyodola pamadyerero,
anandikukutira mano.
17 Hab. 1.13 Ambuye, mudzapenyererabe nthawi yanji?
Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao,
wanga wa wokha kwa misona ya mkango.
18 Mas. 111.1 Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu;
m'chikhamu cha anthu ndidzakulemekezani.
19Adani anga asandikondwerere ine monyenga;
okwiya nane kopanda chifukwa asanditsinzinire.
20Pakuti salankhula zamtendere,
koma apangira chiwembu odekha m'dziko.
21 Mas. 22.13 Ndipo andiyasamira m'kamwa mwao;
nati, Hede, Hede, diso lathu lidachipenya.
22 Mas. 28.1 Yehova, mudazipenya; musakhale chete,
Ambuye, musakhale kutali ndi ine.
23Galamukani, ndipo khalani maso kundiweruzira mlandu wanga,
Mulungu wanga ndi Ambuye wanga.
24 Mas. 26.1 Mundiweruze monga mwa chilungamo chanu,
Yehova Mulungu wanga;
ndipo asandisekerere ine.
25Asanene mumtima mwao, Hede, momwemo!
Asanene, Tammeza iye.
26 Mas. 35.4 Achite manyazi, nadodome iwo akukondwera
chifukwa cha choipa chidandigwera.
Avekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.
27 1Ako. 12.26 Afuule mokondwera nasangalale
iwo akukondwera nacho chilungamo changa,
ndipo anene kosalekeza, Abuke Yehova,
amene akondwera ndi mtendere wa mtumiki wake.
28 Mas. 71.24 Ndipo lilime langa lilalikire chilungamo chanu,
ndi lemekezo lanu tsiku lonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.