LEVITIKO 26 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Malamulo, malonjezo, ndi machenjezo(Deut. 7.12-24; 28.1-68)

1 Mas. 97.7 Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena choimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m'dziko mwanu kuugwadira umenewo; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

2Lev. 19.30Musunge masabata anga, ndi kuchitira ulemu malo anga opatulika; Ine ndine Yehova.

3Mukamayenda m'malemba anga, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita;

4Mas. 85.12; Yow. 2.23; Zek. 8.12ndidzakupatsani mvula m'nyengo zake, ndi dziko lidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'minda idzabala zipatso zake.

5Ndipo nyengo yopuntha tirigu idzafikira nyengo yotchera mphesa, ndi nyengo yotchera mphesa idzafikira nyengo zobzala; ndipo mudzakhuta nacho chakudya chanu, ndi kukhala m'dziko mwanu okhazikika.

6Yes. 2.4; Yob. 11.18-19Ndipo ndidzapatsa mtendere m'dzikomo, kuti mudzagone pansi, wopanda wina wakukuopsani; ndidzaletsanso zilombo zisakhale m'dzikomo, lupanga lomwe silidzapita m'dziko mwanu.

7Mudzapirikitsa adani anu, ndipo adzagwa pamaso panu ndi lupanga.

8Yos. 23.10; Yes. 30.17Asanu a inu adzapirikitsa zana limodzi, ndi zana limodzi la inu adzapirikitsa zikwi khumi; ndi adani anu adzagwa pamaso panu ndi lupanga.

9Ndipo ndidzatembenukira kwa inu, ndi kukubalitsani, ndi kukuchulukitsani; ndipo ndidzakhazika chipangano changa ndinapangana nanucho.

10Ndipo mudzadya za sundwe wakale ndi kutulutsa zakale chifukwa cha zatsopano.

11Ezk. 37.26; Chiv. 21.3Ndidzamanga Kachisi wanga pakati pa inu, ndipo moyo wanga sudzanyansidwa nanu.

122Ako. 6.16Ndipo ndidzayendayenda pakati pa inu, ndi kukhala Mulungu wanu ndi inu mudzakhala anthu anga.

13Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito, kuti musakhale akapolo ao; ndipo ndinathyola mitengo ya magoli anu, ndi kukuyendetsani choweramuka.

14 Mala. 2.2 Koma mukapanda kundimvera Ine, osachita malamulo awa onse;

15ndipo mukakaniza malemba anga, ndi moyo wanu ukanyansidwa nao maweruzo anga, kotero kuti simudzachita malamulo anga onse, koma kuthyola chipangano changa;

16ndidzachitira inu ichinso; ndidzakuikirani zoopsa, nthenda yoondetsa ya m'chifuwa ndi malungo, zakulanda maso ndi mphamvu, ndi kuzunza moyo; ndipo mudzabzala mbeu zanu chabe, popeza adani anu adzazidya.

17Miy. 28.1Ndipo nkhope yanga idzatsutsana nanu; kuti adani anu adzakukanthani, ndipo akudana ndi inu adzachita ufumu pa inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani.

18Ndipo mukapanda kundimvera, zingakhale izi, ndidzaonjeza kukulangani kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu.

19Deut. 28.23Popeza ndidzathyola mphamvu yanu yodzikuza; ndi kusandutsa thambo lanu likhale ngati chitsulo ndi dziko lanu ngati mkuwa;

20Mas. 127.1ndipo mudzachita nayo mphamvu yanu chabe; ndi nthaka yanu siidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'dziko siidzabala zobala zake.

21Ndipo mukayenda motsutsana nane, osalola kumvera Ine; ndidzakuonjezerani miliri kasanu ndi kawiri, monga mwa zochimwa zanu.

22Popeza ndidzatumiza chilombo chakuthengo pakati pa inu, ndipo chidzalanda ana anu, ndi kuononga zoweta zanu ndipo chidzachepetsa inu kuti mukhale pang'ono; ndi njira zanu zidzakhala zakufa.

23Ndipo mukapanda kulangika nazo ndi kubwera kwa Ine, mukayenda motsutsana ndi Ine;

242Sam. 22.27; Mas. 18.26Inenso ndidzayenda motsutsana ndi inu; ndipo ndidzakukanthani Inedi kasanu ndi kawiri chifukwa cha zoipa zanu.

25Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakuchita chilango cha chipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m'mizinda mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m'manja mwa mdani.

26Pamene ndithyola mchirikizo wanu wa mkate, akazi khumi adzaphika mkate wanu mu mchembo umodzi, nadzabweza mkate wanu ndi kuuyesa; ndipo mudzadya, koma osakhuta.

27Ndipo mukapanda kundimvera Ine, chingakhale ichi, ndi kuyenda motsutsana nane;

28Ine ndidzayenda nanu motsutsana mwa kukuzazirani, ndi kukulangani Inedi kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu.

292Maf. 6.28Ndipo mudzadya nyama ya ana anu aamuna; inde nyama ya ana anu aakazi mudzaidya.

302Mbi. 34.7Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu.

31Neh. 2.3Ndipo ndidzasandutsa mizinda yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za fungo lanu lokoma.

32Inde, ndidzapasula dzikoli, ndipo adani anu akukhala m'mwemo adzadabwa nako.

33Mas. 44.11Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja.

34Pamenepo dzikoli lidzakondwera nao masabata ake, masiku onse a kupasuka kwake, pokhala inu m'dziko la adani anu; pamenepo dziko lidzapumula, ndi kukondwera nao masabata ake.

35Masiku onse a kupasuka kwake lipumula; ndiko mpumulo udalisowa m'masabata anu, pokhala inu pamenepo.

36Lev. 26.17Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.

37Ndipo adzakhumudwitsana monga pothawa lupanga, wopanda wakuwalondola; ndipo mudzakhala opanda mphamvu yakuima pamaso pa adani anu.

38Ndipo mudzatayika mwa amitundu, ndi dziko la adani anu lidzakudyani.

39Ndipo otsala mwa inu adzazunzika m'moyo ndi mphulupulu zao m'maiko a adani anu; ndiponso ndi mphulupulu za makolo ao adzazunzika m'moyo.

40Luk. 15.18; 1Yoh. 1.9Pamenepo adzavomereza mphulupulu zao, ndi mphulupulu za makolo ao, pochita zosakhulupirika pa Ine; ndiponso popeza anayenda motsutsana ndi Ine,

41Inenso ndinayenda motsutsana nao, ndi kuwatengera ku dziko la adani ao. Ngati tsono mtima wao wosadulidwa udzichepetsa, ndipo avomereza kulanga kwa mphulupulu zao;

42pamenepo ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo; ndiponso pangano langa ndi Isaki, ndiponso pangano langa ndi Abrahamu ndidzakumbukira; ndipo ndidzakumbukira dzikoli.

43Dziko lomwe lidzasiyidwa nao, ndi kukondwera ndi masabata ake, pokhala lopasuka, iwowa palibe; ndipo iwo adzavomereza kulanga kwa mphulupulu zao; popeza, inde popeza anakaniza maweruzo anga, ndi moyo wao unanyansidwa nao malemba anga.

44Ndiponso pali ichinso: pokhala iwo m'dziko la adani ao sindidzawakaniza, kapena kunyansidwa nao, kuwaononga konse, ndi kuthyola pangano langa ndinapangana nao; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wao.

45Koma chifukwa cha iwo ndidzawakumbukira pangano la makolo ao, amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito pamaso pa amitundu, kuti ndikhale Mulungu wao; Ine ndine Yehova.

46Awa ndi malemba ndi maweruzo ndi malamulo amene Yehova anaika pakati pa Iye ndi ana a Israele m'phiri la Sinai, ndi dzanja la Mose.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help