1Maziko ake ali m'mapiri oyera.
2
koposa zokhalamo zonse za Yakobo.
3 Yes. 60 Mzinda wa Mulungu, inu,
akunenerani zakukulemekezani.
4Ndidzatchula Rahabu ndi Babiloni kwa iwo ondidziwa Ine;
taonani, Filistiya ndi Tiro pamodzi ndi Kusi;
uyu anabadwa komweko.
5Ndipo adzanena za Ziyoni,
uyu ndi uyo anabadwa m'mwemo;
ndipo Wam'mwambamwamba ndiye adzaukhazikitsa.
6 Ezk. 13.9 Yehova adzawerenga, polembera mitundu ya anthu,
uyu anabadwa komweko.
7 Yes. 12.3 Ndipo oimba ndi oomba omwe adzati,
akasupe anga onse ali mwa inu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.