MASALIMO 33 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Alemekeza Mulungu wolenga, wosunga zonse

1 Mas. 32.11; 147.1 Fuulani mokondwera mwa Yehova, inu olungama mtima,

oongoka mtima ayenera kulemekeza.

2Yamikani Yehova ndi zeze;

muimbireni ndi chisakasa cha zingwe khumi.

3 Mas. 96.1; Chiv. 5.9 Mumuimbire Iye nyimbo yatsopano;

muimbe mwaluso kumveketsa mau.

4Pakuti mau a Yehova ali olunjika;

ndi ntchito zake zonse zikhulupirika.

5 Mas. 119.6 Iye ndiye wakukonda chilungamo ndi chiweruzo,

dziko lapansi ladzala ndi chifundo cha Yehova.

6 Gen. 1.6-7, 9 Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova;

ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse.

7Amaunjika madzi a m'nyanja monga mulu,

amakundika zakudya mosungiramo.

8Dziko lonse lapansi liope Yehova,

ponse pali anthu achite mantha chifukwa cha Iye.

9 Gen. 1.3 Pakuti ananena, ndipo chinachitidwa;

analamulira, ndipo chinakhazikika.

10 Yes. 19.3 Yehova aphwanya upo wa amitundu,

asandutsa chabe zolingirira za mitundu ya anthu.

11 Yes. 46.10 Chiweruzo cha Yehova chikhazikika chikhazikikire,

zolingirira za m'mtima mwake ku mibadwomibadwo.

12 Mas. 144.15 Wodalitsika mtundu wa anthu

umene Yehova ndiye Mulungu wao;

mtundu womwe anausankha ukhale cholowa cha Iye yekha.

13Yehova apenyerera m'mwamba;

aona ana onse a anthu.

14M'malo akhalamo Iye, amapenya pansi

pa onse akukhala m'dziko lapansi.

15 Yer. 32.19 Iye amene akonza mitima ya iwo onse,

amene azindikira zochita zao zonse.

16 Mas. 44.6 Palibe mfumu yoti gulu lalikulu limpulumutsa,

mphamvu yaikulu siichilanditsa chiphona.

17 Miy. 21.31 Kavalo safikana kupulumuka naye,

chinkana mphamvu yake njaikulu sapulumutsa.

18 Mas. 34.15 Taonani, diso la Yehova lili pa iwo akumuopa Iye,

pa iwo akuyembekeza chifundo chake.

19Kupulumutsa moyo wao kwa imfa,

ndi kuwasunga ndi moyo m'nyengo ya njala.

20 Mas. 62.1, 5 Moyo wathu walindira Yehova;

Iye ndiye thandizo lathu ndi chikopa chathu.

21 Yoh. 16.22 Pakuti mtima wathu udzakondwera mwa Iye,

chifukwa takhulupirira dzina lake loyera.

22Yehova, chifundo chanu chikhale pa ife,

monga takuyembekezani Inu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help