HABAKUKU Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau OyambaMneneriyu adalalika mau ake pamene Ababiloni adaononga ufumu wa Aasiriya (610-600 BC.). Habakuku akhumudwa poona kuti nawonso ndi anthu ankhanza. Iye anavutika mumtima ndipo anadandaula kwa Mulungu nati, “mupenyereranji iwo akuchita mochenjerera, ndi kukhala chete pamene woipa ammeza munthu wolungama woposa iye mwini” (1.13). Yankho la Mulungu ndi lakuti iye adzachitapo kanthu nthawi itakwana, koma pakadali pano, “wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake” (2.4).Kwinako bukuli likumaliza ndi ndakatulo yotamanda ukulu wa Mulungu ndi kuonetsa chikhulupiriro chosagwedezeka cha mlakatuliyo.Za mkatimuKudandaula kwa Habakuku 1.1—2.4

Tsoka kwa anthu osalungama 2.5-20

Pemphero la Habakuku 3.1-19

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help