NUMERI 1 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Aisraele awerengedwa m'chipululu cha Sinai

1 Eks. 19.1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, m'chihema chokomanako, tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,

2Eks. 30.12; 2Sam. 24.2Werenga khamu lonse la ana a Israele, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba ya makolo ao ndi kuwerenga maina ao, amuna onse mmodzimmodzi.

3Iwe ndi Aroni muwawerenge monga mwa magulu ao, onse mu Israele akutuluka ku nkhondo, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.

4Ndipo pamodzi ndi inu pakhale munthu mmodzi wa mafuko onse; yense mkulu wa nyumba ya kholo lake.

5Ndipo maina a amuna amene aime nanu ndi awa: wa Rubeni, Elizuri mwana wa Sedeuri.

6Wa Simeoni, Selumiele mwana wa Zurishadai.

7Wa Yuda, Nasoni mwana wa Aminadabu.

8Wa Isakara, Netanele mwana wa Zuwara.

9Wa Zebuloni, Eliyabu mwana wa Heloni.

10Wa ana a Yosefe: wa Efuremu, Elisama mwana wa Amihudi; wa Manase, Gamaliele mwana wa Pedazuri.

11Wa Benjamini, Abidani mwana wa Gideoni.

12Wa Dani, Ahiyezere mwana wa Amisadai.

13Wa Asere, Pagiyele mwana wa Okarani.

14Wa Gadi, Eliyasafu mwana wa Deuwele.

15Wa Nafutali, Ahira mwana wa Enani.

16Iwo ndiwo oitanidwa a khamu, akalonga a mafuko a makolo ao; ndiwo akulu a zikwizo za Israele.

17Ndipo Mose ndi Aroni anatenga anthu awa, onenedwa maina ao;

18nasonkhanitsa khamu lonse tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, ndipo iwo anawakumbira magwero ao kutchula mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao, ndi kuwerenga maina kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mmodzimmodzi.

19Monga Yehova analamula Mose, momwemo anawawerenga m'chipululu cha Sinai.

20Ndipo ana a Rubeni, mwana woyamba wa Israele, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina mmodzimmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

21owerengedwa ao a fuko la Rubeni, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu.

22A ana a Simeoni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, owerengedwa ao, powerenga maina mmodzimmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

23owerengedwa ao a fuko la Simeoni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi zinai kudza mazana atatu.

24A ana a Gadi, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

25owerengedwa ao a fuko la Gadi, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu.

26A ana a Yuda, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

27owerengedwa ao a fuko la Yuda, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zinai kudza mazana asanu ndi limodzi.

28A ana a Isakara, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

29owerengedwa ao a fuko la Isakara, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zinai kudza mazana anai.

30A ana a Zebuloni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

31owerengedwa ao a fuko la Zebuloni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai.

32A ana a Yosefe, ndiwo a ana a Efuremu, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

33owerengedwa ao a fuko la Efuremu, ndiwo zikwi makumi anai mphambu mazana asanu.

34A ana a Manase, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

35owerengedwa ao a fuko la Manase, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana awiri.

36A ana a Benjamini, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

37owerengedwa ao a fuko la Benjamini, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai.

38A ana a Dani, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

39owerengedwa ao a fuko la Dani, ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.

40A ana a Asere, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

41owerengedwa ao a fuko la Asere, ndiwo zikwi makumi anai mphambu chimodzi kudza mazana asanu.

42A ana a Nafutali, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;

43owerengedwa ao a fuko la Nafutali, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.

44Iwo ndiwo amene anawerengedwa, amene Mose anawerenga pamodzi ndi Aroni, ndi akalonga a Israele, ndiwo amuna khumi ndi awiri; yense kunenera nyumba ya kholo lake.

45Potero owerengedwa onse a ana a Israele monga mwa nyumba za makolo ao, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo mu Israele;

46inde owerengedwa onse ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.

Alevi sawerengedwa

47Koma Alevi monga mwa fuko la makolo ao sanawerengedwe mwa iwo.

48Popeza Yehova adalankhula ndi Mose, ndi kuti,

49Fuko la Levi lokha usaliwerenge, kapena kuona kufikira kwao mwa ana a Israele;

50Eks. 38.21; Num. 3.23, 38koma iwe, uike Alevi asunge chihema cha mboni, ndi zipangizo zake zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula chihema, ndi zipangizo zake zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa chihema.

51Num. 10.17Ndipo akati amuke nacho chihemacho, Alevi amgwetse, ndipo akati achimange, Alevi achiimike; ndipo mlendo akayandikizako amuphe.

52Ndipo ana a Israele amange mahema ao, yense ku chigono chake, ndi yense ku mbendera yake, monga mwa makamu ao.

532Mbi. 13.11Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni.

54Momwemo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose; anachita momwemo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help