OWERUZA Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau OyambaBukuli likukamba zochitika zina ndi zina kuyambira nthawi imene Aisraele analowa m'dziko la Kanani kufikira nthawi yokhazikitsa ufumu. Pa nthawi yonseyo Aisraele anakhala akuzunzika kwambiri chifukwa chokhala pakati pa anthu a mitundu ina, anthu ofunkha ndi ankhanza, kotero kuti panali chisokonezo. Bukuli litchedwa Oweruza, kunena anthu angapo amene Yehova awaitana kuti azitsogolera Aisraele anzao pa nkhondo yomenyana ndi adani. Woweruza wina wodziwika kwambiri ndi Samisoni amene zochita zake zikukambidwa pamutu 13 mpaka 16.Phunziro lopezeka m'bukuli ndilo lakuti, Israele akakhala okhulupirika kwa Yehova, amakhala pa mtendere. Koma akafulatira Mulungu ndi kumamchimwira, amagwa m'mavuto aakulu. Komabe ngakhale iwo apandukira Yehova ndi kugwa m'mavuto, Mulungu ali wokonzeka kuwapulumutsa anthu akewo, ataona kuti atembenuka ndi kubwerera kwa Iyeyo.Za mkatimuZochitika zina kufikira nthawi ya imfa ya Yoswa 1.1—2.10

Za oweruza ena ndi ena 2.11—16.31

Zochitika zinanso 17.1—21.25

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help