1
35Mac. 13.1Koma Paulo ndi Barnabasi anakhalabe mu Antiokeya, nalinkuphunzitsa, ndi kulalikira mau a Ambuye pamodzi ndi ena ambiri.
Paulo ndi Barnabasi alekana36 Mac. 13—14 Patapita masiku, Paulo anati kwa Barnabasi, Tibwerere, tizonde abale m'mizinda yonse m'mene tinalalikiramo mau a Ambuye, tione mkhalidwe wao.
37Mac. 12.12, 25; 13.5, 13; 2Tim. 4.11Ndipo Barnabasi anafuna kumtenga Yohane uja, wotchedwa Marko
38Koma sikunamkomere Paulo kumtenga iye amene anawasiya nabwerera pa Pamfiliya paja osamuka nao kuntchito.
39Ndipo panali kupsetsana mtima, kotero kuti analekana wina ndi mnzake; ndipo Barnabasi anatenga Marko, nalowa m'ngalawa, nanka ku Kipro.
Ulendo wachiwiri wa Paulo40 Mac. 14.26 Koma Paulo anasankha Silasi, namuka, woikizidwa ndi abale ku chisomo cha Ambuye.
41Mac. 16.5Ndipo iye anapita kupyola pa Siriya ndi Silisiya, nakhazikitsa Mipingo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.