1Ndipo m'masiku a Davide munali njala, zaka zitatu; ndipo Davide anafunsira kwa Yehova. Ndipo Yehova anati, Ndicho chifukwa cha Saulo ndi nyumba yake yamwazi, popeza iye anawapha Agibiyoni.
2Yos. 9.3, 15-17Ndipo mfumu inaitana Agibiyoni, ninena nao (koma Agibiyoni, sanali a ana a Israele, koma a Aamori otsala; ndipo ana a Israele anawalumbirira kwa iwo, koma Saulo anafuna kuwapha mwa changu chake cha kwa ana a Israele ndi a Yuda).
3Ndipo Davide ananena ndi Agibiyoni, Ndidzakuchitirani chiyani, ndipo ndidzakuyanjanitsani ndi chiyani kuti mukadalitse cholowa cha Yehova?
4Ndipo Agibiyoni ananena naye, Sitifuna siliva kapena golide wa Saulo kapena nyumba yake; ndiponso sitifuna kupha munthu aliyense wa mu Israele. Nati iye, Monga inu mudzanena, momwemo ndidzakuchitirani.
5Ndipo anati kwa mfumu, Munthu uja anatitha natilingalira pa ife chotionongera kuti tisakhalenso m'malire ali onse a Israele.
61Sam. 10.24Mutipatse ana ake aamuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapachika kwa Yehova mu Gibea wa Saulo, wosankhika wa Yehova. Mfumu niti, Ndidzawapereka.
71Sam. 20.42Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Yonatani mwana wa Saulo.
8Koma mfumu inatenga ana aamuna awiri a Rizipa mwana wamkazi wa Aya, amene anambalira Saulo, ndiwo Arimoni ndi Mefiboseti; ndiponso ana aamuna asanu a Mikala, mwana wamkazi wa Saulo, amene iye anambalira Adriyele mwana wa Barizilai Mmehola;
9niwapereka m'manja a Agibiyoni, iwo nawapachika m'phiri pamaso pa Yehova, ndipo anagwa pamodzi onse asanu ndi awiri; m'masiku a kukolola, m'masiku oyamba, poyamba kucheka barele.
10Ndipo Rizipa mwana wamkazi wa Aya anatenga chiguduli, nadziyalira ichi pathanthwe, kuyambira pakukolola kufikira madzi ochokera kumwamba adawagwera; ndipo sadalole mbalame za m'mlengalenga kutera pa iwo usana, kapena zilombo zakuthengo usiku.
11Ndipo anauza Davide chimene Rizipa mwana wamkazi wa Aya, mkazi wamng'ono wa Saulo anachita.
121Sam. 31.10-13Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi amene anawaba m'khwalala la Beteseani, kumene Afilisti adawapachika, tsiku lija Afilistiwo anapha Saulo ku Gilibowa;
13nachotsa kumeneko mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake; nasonkhanitsa iwo mafupa a iwo aja adapachikidwa.
14Yos. 7.26Naika mafupa a Saulo ndi Yonatani mwana wake ku dziko la Benjamini mu Zela, m'manda a Kisi atate wake; nachita zonse inalamulira mfumu. Ndipo pambuyo pake Mulungu anapembedzeka za dzikolo.
Nkhondo zakupha ziphona za Afilisti(1Mbi. 20.4-8)15Ndipo Afilisti anaponyananso nkhondo ndi Aisraele; ndipo Davide anatsika ndi anyamata ake pamodzi naye naponyana ndi Afilisti; nafuna kukomoka Davide.
16Ndipo Isibi-Benobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wake kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anavala lupanga latsopano, nati aphe Davide.
172Sam. 18.3; 1Maf. 11.36Koma Abisai mwana wa Zeruya anamthandiza namkantha Mfilistiyo, namupha. Pomwepo anthu a Davide anamlumbirira iye nati, Inu simudzatuluka nafenso kunkhondo, kuti mungazime nyali ya Israele.
18Ndipo kunali chitapita ichi, kunalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; pamenepo Sibekai Muhusa anapha Safi, ndiye wa ana a Rafa.
19Ndipo panalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; ndipo Elihanani mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliyati Mgiti, amene mtengo wa mkondo wake unanga mtanda wa woombera nsalu.
20Ndipo panalinso nkhondo ku Gati, kumene kunali munthu wa msinkhu waukulu, amene anali nazo zala zisanu ndi chimodzi padzanja lonse, ndi pa phazi lonse zala zisanu ndi chimodzi, kuwerenga kwa zonse ndiko makumi awiri ndi zinai; ndipo iyenso anambala ndi Rafa.
21Ndipo pakutonza Israele iyeyu, Yonatani mwana a Simea mbale wa Davide anamupha.
221Mbi. 20.8Awa anai anawabala ndi Rafa ku Gati; ndipo anagwa ndi dzanja la Davide ndi la anyamata ake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.