1 Mac. 10.42 Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa, ndi pa maonekedwe ake ndi ufumu wake;
21Tim. 5.20lalikira mau; chita nao pa nthawi yake, popanda nthawi yake; tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.
32Tim. 3.1Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; komatu poyabwa m'khutu adzadziunjikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha:
4ndipo adzalubza dala pachoonadi, nadzapatukira kutsata nthano zachabe.
5Mac. 21.8; 2Tim. 2.3Koma iwe, khala maso m'zonse, imva zowawa, chita ntchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako.
Paulo azindikira kuti imfa yake mpafupi. Aitana Timoteo amzonde. Mbiri ya Dema ndi ena6 Afi. 1.23; 2.17 Pakuti ndilimkuthiridwa nsembe tsopano, ndipo nthawi ya kumasuka kwanga yafika.
71Tim. 6.12Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro:
81Ako. 9.25chotsalira wandiikira ine korona wa chilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anakonda maonekedwe ake.
9Tayesetsa kudza kwa ine msanga:
10Akol. 4.14; 1Yoh. 2.15pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, napita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalamatiya.
11Mac. 15.37; Akol. 4.14Luka yekha ali pamodzi ndi ine. Umtenge Marko, adze pamodzi ndi iwe; pakuti ayenera kunditumikira.
12Aef. 6.21Koma Tikiko ndamtuma ku Efeso.
13Chofunda chija ndinachisiya ku Troasi kwa Karpo, udze nacho pakudza iwe, ndi mabuku, makamaka zikopa zija zolembedwa.
141Tim. 1.20Aleksandro wosula mkuwa anandichitira zoipa zambiri: adzambwezera iye Ambuye monga mwa ntchito zake;
15ameneyo iwenso uchenjere naye; pakuti anatsutsana nao mau athu.
16Mac. 7.60; 2Tim. 1.15Pa chodzikanira changa choyamba panalibe mmodzi anandithangata, koma onse anandisiya; chimenecho chisawerengedwe chowatsutsa.
17Mat. 10.19; Aef. 3.8Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.
18Mas. 121.7; Aro. 11.36Ambuye adzandilanditsa ku ntchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kulowa Ufumu wake wa Kumwamba; kwa Iye ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.
19 Mac. 18.2; 2Tim. 1.16 Pereka moni kwa Prisika ndi Akwila, ndi banja la Onesifore.
20Mac. 19.22; 21.29Erasto anakhalira mu Korinto; koma Trofimo ndamsiya wodwala ku Mileto.
212Tim. 4.9Tayesetsa kudza isanadze nyengo yachisanu. Akukupatsa moni Yubulo, ndi Pude, ndi Lino, ndi Klaudia, ndi abale onse.
22 Agal. 6.18 Ambuye akhale ndi mzimu wako. Chisomo chikhale nanu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.