1Ndipo ana a Israele monga mwa chiwerengo chao, kunena za akulu a nyumba za makolo ao, ndi akazembe a zikwi, ndi a mazana, ndi akapitao ao akutumikira mfumu mu ntchito iliyonse ya magawidwe, akulowa ndi kutuluka mwezi ndi mwezi, miyezi yonse ya chaka, chigawo chilichonse ncha amuna zikwi makumi awiri mphambu zinai.
22Sam. 23.8; 1Mbi. 11.11Woyang'anira chigawo choyamba cha mwezi, woyamba ndiye Yasobeamu mwana wa Zabidiele; m'chigawo mwake munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.
3Ndiye wa ana a Perezi, mkulu wa akazembe onse a khamu mwezi woyamba.
4Woyang'anira chigawo cha mwezi wachiwiri ndiye Dodai Mwahohi ndi chigawo chake; ndi Mikiloti mtsogoleri, ndi m'chigawo chake munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.
5Kazembe wachitatu wa khamu wa mwezi wachitatu ndiye Benaya mwana wa Yehoyada wansembe wamkulu; ndi m'chigawo mwake munalinso zikwi makumi awiri mphambu zinai.
6Benaya ameneyo ndiye wamphamvu uja wa makumi atatu aja, woyang'anira chigawo chake ndi Amizabadi mwana wake.
7Wachinai wa mwezi wachinai ndiye Asahele mbale wa Yowabu, ndi pambuyo pake Zebadiya mwana wake; ndi m'chigawo mwake munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.
8Kazembe wachisanu wa mwezi wachisanu ndiye Samuti Mwizara; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.
9Wachisanu ndi chimodzi wa mwezi wachisanu ndi chimodzi ndiye Ira mwana wa Ikesi Mtekowa; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.
10Wachisanu ndi chiwiri wa mwezi wachisanu ndi chiwiri ndiye Helezi Mpeloni wa ana a Efuremu; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.
11Wachisanu ndi chitatu wa mwezi wachisanu ndi chitatu ndiye Sibekai Muhusa wa Azera; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.
12Wachisanu ndi chinai wa mwezi wachisanu ndi chinai ndiye Abiyezere Mwanatoti wa Abenjamini; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.
13Wakhumi wa mwezi wakhumi ndiye Maharai Mnetofa wa Azera; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.
14Wakhumi ndi chimodzi wa mwezi wakhumi ndi chimodzi ndiye Benaya Mpiratoni wa ana a Efuremu; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.
15Wakhumi ndi chiwiri wa mwezi wakhumi ndi chiwiri ndiye Helidai Mnetofa wa Otiniyele; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.
Oyang'anira mafuko 12 a Israele16Koma oyang'anira mafuko a Israele ndi awa: wa Arubeni mtsogoleri wao ndiye Eliyezere mwana wa Zikiri; wa Asimeoni, Sefatiya mwana wa Maaka;
17wa Alevi, Hasabiya mwana wa Kemuwele; wa Aroni, Zadoki;
18wa Yuda, Elihu mbale wina wa Davide; wa Isakara, Omuri mwana wa Mikaele;
19wa Zebuloni, Isimaya mwana wa Obadiya; wa Nafutali, Yerimoti mwana wa Aziriele;
20wa ana a Efuremu, Hoseya mwana wa Azaziya; wa hafu la fuko la Manase, Yowele mwana wa Pedaya;
21wa hafu la fuko la Manase mu Giliyadi, Ido mwana wa Zekariya; wa Benjamini, Yaasiyele mwana wa Abinere;
22wa Dani, Azarele mwana wa Yerohamu. Awa ndi akazembe a mafuko a Israele.
23Gen. 15.5Koma Davide sanawerenge iwo a zaka makumi awiri ndi ochepapo, pakuti Yehova adati kuti adzachulukitsa Israele ngati nyenyezi za kuthambo.
241Mbi. 21.17; 2Sam. 24.12, 15Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga, koma sanatsirize; ndi mkwiyo unagwera Israele chifukwa cha ichi, ndipo chiwerengo chao sichinalembedwe m'buku la mbiri ya mfumu Davide.
Oyang'anira a zake za Davide25Ndipo woyang'anira chuma cha mfumu ndiye Azimaveti mwana wa Adiyele, ndi woyang'anira wa chuma cha m'minda, m'mizinda ndi m'midzi, ndi nyumba za nsanja, ndiye Yonatani mwana wa Uziya;
26ndi woyang'anira iwo akugwira ntchito ya m'munda yakulima nthaka ndiye Eziri mwana wa Kelubu;
27ndi woyang'anira minda yampesa ndiye Simei Mramati; ndi woyang'anira zipatso za minda yampesa zisungike mosungiramo vinyo ndiye Zabidi Msifamu;
28ndi woyang'anira mitengo ya azitona, ndi yamikuyu yokhala kuzidikha kunsi, ndiye Baala-Hanani Mgederi; ndi woyang'anira zosungiramo mafuta ndiye Yowasi;
29ndi woyang'anira ng'ombe zakudya mu Saroni ndiye Sitirai Msaroni; ndi woyang'anira ng'ombe za m'zigwa ndiye Safati mwana wa Adilai;
30ndi woyang'anira ngamira ndiye Obili Mwismaele; ndi woyang'anira abulu ndiye Yedeiya Mmeronoti;
31ndi woyang'anira zoweta zazing'ono ndiye Yazizi Mhagiri. Onsewa ndiwo akulu a zolemera zake za mfumu Davide.
32Ndipo Yonatani atate wake wina wa Davide anali phungu, munthu wanzeru ndi mlembi; ndi Yehiyele mwana wa Hakimoni anakhala ndi ana a mfumu;
332Sam. 15.12, 37ndi Ahitofele anali phungu wa mfumu, ndi Husai Mwariki anali bwenzi la mfumu;
342Sam. 20.23, 25ndi wotsatana ndi Ahitofele, Yehoyada mwana wa Benaya, ndi Abiyatara; koma kazembe wa nkhondo ya mfumu ndiye Yowabu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.