1 Ezk. 47.1 Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka kumpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.
2Ezk. 47.12Pakati pa khwalala lake, ndi tsidya ili la mtsinje, ndi tsidya lake lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziwiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nao amitundu.
3Ezk. 48.35; Zek. 14.11Ndipo sipadzakhalanso temberero lililonse; ndipo mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa udzakhala momwemo; ndipo akapolo ake adzamtumikira Iye,
4Chiv. 14.1nadzaona nkhope yake; ndipo dzina lake lidzakhala pamphumi pao.
52Tim. 2.12; Chiv. 21.23, 25Ndipo sikudzakhalanso usiku; ndipo sasowa kuunika kwa nyali, ndi kuunika kwa dzuwa; chifukwa Ambuye Mulungu adzawaunikira; ndipo adzachita ufumu kunthawi za nthawi.
Machenjezo ndi malonjezano6Ndipo anati kwa ine, Mau awa ali okhulupirika ndi oona; ndipo Ambuye, Mulungu wa mizimu ya aneneri, anatuma mngelo wake kukaonetsera akapolo ake zimene ziyenera kuchitika msanga.
7Chiv. 1.3; 3.11Ndipo taonani, ndidza msanga. Wodala iye amene asunga mau a chinenero cha buku ili.
8 Chiv. 19.10 Ndipo ine Yohane ndine wakumva ndi wakupenya izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kupenya, ndinagwa pansi kulambira pa mapazi a mngelo wakundionetsa izo.
9Chiv. 19.10Ndipo ananena kwa ine, Tapenya, usachite; ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga mau a buku ili; lambira Mulungu.
10 Dan. 8.26; Chiv. 1.3 Ndipo ananena ndi ine, Usasindikiza chizindikiro mau a chinenero cha buku ili; pakuti nthawi yayandikira.
112Tim. 3.13Iye wakukhala wosalungama achitebe zosalungama; ndi munthu wonyansa akhalebe wonyansa; ndi iye wakukhala wolungama achitebe cholungama; ndi iye amene ali woyera akhalebe woyeretsedwa.
12Yes. 40.10; Chiv. 20.12; 22.7Taonani, ndidza msanga; ndipo mphotho yanga ndili nayo yakupatsa yense monga mwa ntchito yake.
13Chiv. 1.8, 11Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Chitsiriziro.
14Chiv. 22.2Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m'mzinda pazipata.
151Ako. 6.9-10; Chiv. 9.20-21; 21.8Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.
16 Chiv. 1.1; 2.28; 5.5 Ine Yesu ndatuma mngelo wanga kukuchitirani umboni za izi m'Mipingo. Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide, nyenyezi yonyezimira ya nthanda.
17 Yes. 55.1; Chiv. 21.2, 9 Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.
18 Deut. 4.2 Ndichita umboni kwa munthu aliyense wakumva mau a chinenero cha buku ili, Munthu akaonjeza pa awa, adzamuonjezera Mulungu miliri yolembedwa m'bukumu:
19Deut. 4.2; Chiv. 21.2ndipo aliyense akachotsako pa mau a buku la chinenero ichi, Mulungu adzamchotsera gawo lake pa mtengo wa moyo, ndi m'mzinda woyerawo, ndi pa izi zilembedwa m'bukumu.
20 Chiv. 22.12 Iye wakuchitira umboni izi, anena, Indetu; ndidza msanga. Amen; idzani, Ambuye Yesu.
21 2Ate. 3.18 Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi oyera mtima onse. Amen.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.