1 Mas. 121.1; 11.4 Ndikweza maso anga kwa Inu,
kwa Inu wakukhala kumwamba.
2Taonani, monga maso a anyamata
ayang'anira dzanja la mbuye wao,
monga maso a adzakazi
ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi:
Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu,
kufikira atichitira chifundo.
3Mutichitire chifundo, Yehova, mutichitire chifundo;
pakuti takhuta kwambiri ndi mnyozo.
4Moyo wathu wakhuta ndithu
ndi kuseka kwa iwo osasowa kanthu,
ndi mnyozo wa odzikuza.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.