1 Eks. 13.3 M'mene Israele anatuluka ku Ejipito,
nyumba ya Yakobo kwa anthu a chinenedwe chachilendo;
2 Eks. 19.6 Yuda anakhala malo ake oyera, Israele ufumu wake.
3 Eks. 14.21; Yos. 3.13, 16 Nyanjayo inaona, nithawa;
Yordani anabwerera m'mbuyo.
4 Mas. 29.6 Mapiri anatumphatumpha ngati nkhosa zamphongo,
timapiri ngati anaankhosa.
5Unathawanji nawe, nyanja iwe?
Unabwereranji m'mbuyo, Yordani iwe?
6 Mas. 29.6 Munatumphatumphiranji ngati nkhosa zamphongo, mapiri inu?
Ngati anaankhosa, zitunda inu?
7Unjenjemere, dziko lapansi iwe, pamaso pa Ambuye,
pamaso pa Mulungu wa Yakobo;
8 Eks. 17.6 amene anasanduliza thanthwe likhale thawale lamadzi,
nsangalabwi ikhale kasupe wamadzi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.