1 Gen. 39.2 Ndipo Solomoni mwana wa Davide analimbikitsidwa m'ufumu wake, ndipo Yehova Mulungu wake anali naye, namkuza kwakukulu.
2Ndipo Solomoni analankhula ndi Aisraele onse, ndi akulu a zikwi ndi a mazana, ndi kwa oweruza, ndi kwa kalonga aliyense wa Israele, akulu a nyumba za makolo.
31Maf. 3.4Ndipo Solomoni ndi khamu lonse pamodzi naye anamuka ku msanje wa ku Gibiyoni; pakuti kumeneko kunali chihema chokomanako cha Mulungu adachimanga Mose mtumiki wa Yehova m'chipululu.
42Sam. 6.2-17Koma likasa la Mulungu Davide adakwera nalo kuchokera ku Kiriyati-Yearimu kunka kumene Davide adalikonzeratu malo; pakuti adaliutsiratu hema ku Yerusalemu.
5Eks. 27.1-2Guwa la nsembe lomwe lamkuwa, adalipanga Bezalele mwana wa Uri mwana wa Huri linali komweko, ku khomo la Kachisi wa Yehova; ndipo Solomoni ndi khamulo anafunako.
61Maf. 3.5-14Nakwerako Solomoni ku guwa la nsembe pamaso pa Yehova linali ku chihema chokomanako, napereka pamenepo nsembe zopsereza chikwi chimodzi.
Solomoni apempha nzeru kwa Mulungu7Usiku womwewo Mulungu anaonekera kwa Solomoni, nati kwa iye, Pempha chomwe ndikupatse.
8Nati Solomoni kwa Mulungu, Mwachitira Davide atate wanga zokoma zambiri, ndipo mwandiika mfumu m'malo mwake.
9Tsopano, Yehova Mulungu, likhazikike lonjezano lanu la kwa Davide atate wanga; pakuti mwandiika mfumu ya anthu akuchuluka ngati fumbi lapansi.
10Mundipatse tsono nzeru ndi chidziwitso, kuti ndituluke ndi kulowa pamaso pa anthu awa; pakuti angathe ndani kuweruza anthu anu awa ambiri?
11Ndipo Mulungu anati kwa Solomoni, Popeza chinali mumtima mwako ichi, osapempha chuma, akatundu, kapena ulemu, kapena moyo wa iwo akudana nawe, osapemphanso masiku ambiri; koma wadzipemphera nzeru ndi chidziwitso, kuti uweruze anthu anga amene ndakuika ukhale mfumu yao,
12nzeru ndi chidziwitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso chuma, ndi akatundu, ndi ulemu, zotere zonga sanakhale nazo mafumu akale usanakhale iwe, ndi akudza pambuyo pako sadzakhala nazo zotero.
13Momwemo Solomoni anadza ku Yerusalemu kuchokera ku msanje uli ku Gibiyoni, ku khomo la chihema chokomanako; ndipo anachita ufumu pa Israele.
Magaleta ndi apakavalo a Solomoni14 1Maf. 4.26 Ndipo Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi apakavalo, nakhala nao magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'midzi ya magaleta ndi kwa mfumu ku Yerusalemu.
151Maf. 10.27-29Ndipo mfumu inatero kuti siliva ndi golide zikhale m'Yerusalemu ngati miyala, ndi kuti mikungudza ichuluke ngati mikuyu yokhala kuchidikha.
16Ndi akavalo amene Solomoni anali nao anafuma ku Ejipito; amalonda a mfumu anawalandira magulumagulu, gulu lililonse mtengo wake.
17Ndipo anatenga natuluka nalo galeta ku Ejipito mtengo wake masekeli a siliva mazana asanu ndi limodzi, ndi kavalo mtengo wake zana limodzi mphambu makumi asanu; momwemo anawatulutsira mafumu onse a Ahiti, ndi mafumu a Aramu, ndi dzanja lao.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.