1Tcherani khutu pemphero langa, Mulungu;
ndipo musadzibisa pa kupemba kwanga.
2 Yes. 38.14 Mverani, ndipo mundiyankhe,
ndiliralira m'kudandaula kwanga ndi kubuula;
3 2Sam. 16.7-8 chifukwa cha mau a mdani,
chifukwa cha kundipsinja woipa;
pakuti andisenza zopanda pake,
ndipo adana nane mumkwiyo.
4 Mas. 116.3 Mtima wanga uwawa m'kati mwanga;
ndipo zoopsa za imfa zandigwera.
5Mantha ndi kunjenjemera zandidzera,
ndipo zoopsetsa zandikuta.
6Ndipo ndinati, Ha, wina akadandipatsa mapiko onga a njiwa!
Mwenzi nditauluka, ndi kukhaliratu.
7Onani, ndikadathawira kutali,
ndikadagona m'chipululu.
8Ndikadafulumira ndipulumuke
kumphepo yolimba ndi namondwe.
9Aonongeni, Ambuye, gawani lilime lao,
pakuti ndaona chiwawa ndi ndeu m'mudzimo.
10Izizo ziuzungulira pa malinga ake usana ndi usiku;
ndipo m'kati mwake muli zopanda pake ndi chovuta.
11M'kati mwake muli kusakaza,
chiwawa ndi chinyengo sizichoka m'makwalala ake.
12 Mas. 41.9 Pakuti si mdani amene ananditonzayo;
pakadatero ndikadachilola,
amene anadzikuza pa ine sindiye munthu wondida;
pakadatero ndikadambisalira:
13Koma ameneyo ndiwe, munthu woyenerana nane,
tsamwali wanga, wodziwana nane.
14 Mas. 42.4 Tinapangirana upo wokoma,
tinaperekeza khamu la anthu popita kunyumba ya Mulungu.
15Imfa iwagwere modzidzimutsa,
atsikire kumanda ali amoyo,
pakuti m'mokhala mwao muli zoipa pakati pao.
16Koma ine ndidzafuulira kwa Mulungu;
ndipo Yehova adzandipulumutsa.
17Madzulo, m'mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula,
ndipo adzamva mau anga.
18Anaombola moyo wanga kunkhondo yondilaka,
ndikhale mumtendere,
pakuti ndiwo ambiri okangana nane.
19 Deut. 33.27 Mulungu adzamva, nadzawasautsa,
ndiye wokhalabe chiyambire kale lomwe.
Popeza iwowa sasinthika konse,
ndipo saopa Mulungu.
20Anatulutsa manja ake awagwire iwo akuyanjana naye,
anaipsa pangano lake.
21 Miy. 5.3-4 Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka,
koma mumtima mwake munali nkhondo,
mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga,
koma anali malupanga osololasolola.
22 Luk. 12.22; Afi. 4.6; 1Pet. 5.7 Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza,
nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.
23 Miy. 10.27 Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko.
Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu;
koma ine ndidzakhulupirira Inu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.