1 MBIRI 9 - Buku Lopatulika Bible 2014

Okhala m'Yerusalemu atabwera kuchokera ku Babiloni

1 Ezr. 2.59 Ndipo Aisraele onse anawerengedwa mwa chibadwidwe chao; ndipo taonani, alembedwa m'buku la mafumu a Israele; ndipo Yuda anatengedwa ndende kunka ku Babiloni chifukwa cha kulakwa kwao.

2Yos. 9.27; Ezr. 2.70Okhala m'dziko oyamba tsono, akukhala mwaomwao m'midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, Alevi, ndi Anetini.

3Neh. 11.1Ndipo m'Yerusalemu munakhala a ana a Yuda, ndi a ana a Benjamini, ndi a ana a Efuremu ndi Manase:

4Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omuri, mwana wa Imuri, mwana wa Bani, wa ana a Perezi mwana wa Yuda.

5Ndipo a Asiloni: Asaya woyamba, ndi ana ake.

6Ndi a ana a Zera: Yeuwele ndi abale ao mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi anai.

7Ndi a ana a Benjamini: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Hodaviya, mwana wa Hasenuwa;

8ndi Ibineya mwana wa Yerohamu, ndi Ela mwana wa Uzi, mwana wa Mikiri, ndi Mesulamu mwana wa Sefatiya, mwana wa Reuwele, mwana wa Ibineya,

9ndi abale ao monga mwa mibadwo yao mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi. Onsewa ndiwo akulu a nyumba za makolo ao m'nyumba za makolo ao.

10Ndi a ansembe: Yedaya, ndi Yehoyaribu, ndi Yakini,

11ndi Azariya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Meraiyoti, mwana wa Ahitubi, mtsogoleri wa m'nyumba ya Mulungu;

12ndi Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pasuri, mwana wa Malikiya, ndi Maasai mwana wa Adiyele, mwana wa Yazera, mwana wa Mesulamu, mwana wa Mesilemiti, mwana wa Imeri,

13ndi abale ao, akulu a nyumba za makolo ao chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi limodzi, anthu odziwitsitsa ntchito ya utumiki wa nyumba ya Mulungu.

14Ndi a Alevi: Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, a ana a Merari;

15ndi Bakibakara, Heresi, ndi Galali, ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zikiri, mwana wa Asafu;

16ndi Obadiya mwana wa Semaya, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni, ndi Berekiya mwana wa Asa, mwana wa Elikana, wokhala m'midzi ya Anetofa.

17Ndi odikira pakhomo: Salumu, ndi Akubu, ndi Talimoni, ndi Ahimani ndi abale ao; Salumu ndi mkulu wao,

18amene adadikira pa chipata cha mfumu kum'mawa mpaka pomwepo, ndiwo odikira pakhomo a tsasa la ana a Levi.

19Ndipo Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, ndi abale ake a nyumba ya atate wake; Akora anayang'anira ntchito ya utumiki, osunga zipata za Kachisi monga makolo ao; anakhala m'chigono cha Yehova osunga polowera;

20Num. 31.6ndi Finehasi mwana wa Eleazara anali mtsogoleri wao kale, ndipo Yehova anali naye.

21Zekariya mwana wa Meselemiya anali wodikira pakhomo pa chihema chokomanako.

22Iwo onse osankhidwa akhale odikira kuzipata ndiwo mazana awiri mphambu khumi ndi awiri. Iwo anawerengedwa monga mwa chibadwidwe chao, m'midzi mwao, amene Davide ndi Samuele mlauli anawaika m'udindo wao.

23Momwemo iwo ndi ana ao anayang'anira zipata za kunyumba ya Yehova, ndiyo nyumba ya Kachisi, m'udikiro wao.

24Pa mbali zinai panali odikira kum'mawa, kumadzulo, kumpoto, ndi kumwera.

25Ndi abale ao m'midzi mwao akafikafika, atapita masiku asanu ndi awiri masabata onse, kuti akhale nao;

26pakuti odikira anai akulu, ndiwo Alevi, anali m'udindo wao, nayang'anira zipinda ndi mosungiramo chuma m'nyumba ya Mulungu.

27Ndipo amagona usiku m'zipinda zozinga nyumba ya Mulungu, popeza udikiro wake ndi wao; kuitsegula m'mawa ndi m'mawa ndi kwaonso.

28Ndi ena a iwo anayang'anira zipangizo za utumikiwo, pakuti analowa nazo ataziwerenga, natuluka nazo ataziwerenga.

29Ndi ena a iwo anaikidwa ayang'anire zipangizo zilizonse, ndi zipangizo zonse za malo opatulika, ndi ufa wosalala, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi lubani, ndi zonunkhira.

30Eks. 30.22-25Ndi ana ena a ansembe anasanganiza chisanganizo cha zonunkhira.

31Lev. 2.5Ndi Matitiya wina wa Alevi, ndiye mwana woyamba wa Salumu Mkora, anaikidwa ayang'anire zokazingidwa m'ziwaya.

32Lev. 24.5-8Ndi ena a abale ao, a ana a Akohati, anayang'anira mkate woonekera, kuukonza masabata onse.

331Mbi. 6.31; 25.1; Mas. 134.1Ndipo awa ndi oimba akulu a nyumba za makolo a Alevi, okhala m'zipinda, omasuka ku ntchito zina; pakuti anali nayo ntchito yao usana ndi usiku.

34Awa ndi akulu a nyumba za makolo a Alevi mwa mibadwo yao, ndiwo akulu; anakhala ku Yerusalemu awa.

35Ndipo m'Gibiyoni munakhala atate wa Gibiyoni Yeiyele, dzina la mkazi wake ndiye Maaka;

36ndi mwana wake woyamba ndiye Abidoni, opondana naye ndi Zuri, ndi Kisi, ndi Baala, ndi Nere, ndi Nadabu,

37ndi Gedori, ndi Ahiyo, ndi Zekariya, ndi Mikiloti.

38Ndi Mikiloti anabala Simeamu. Ndipo iwonso anakhala pamodzi ndi abale ao m'Yerusalemu, pandunji pa abale ao.

391Mbi. 8.33Ndipo Nere anabala Kisi, ndi Kisi anabala Saulo, ndi Saulo anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esibaala.

40Ndipo mwana wa Yonatani ndiye Meribaala; ndi Meribaala anabala Mika.

41Ndi ana a Mika: Pitoni, ndi Meleki, ndi Tareya, ndi Ahazi.

42Ndi Ahazi anabala Yara, ndi Yara anabala Alemeti, ndi Azimaveti, ndi Zimiri; ndi Zimiri anabala Moza,

43ndi Moza anabala Bineya, ndi Refaya mwana wake, Eleasa mwana wake, Azele mwana wake;

44ndi Azele anali nao ana asanu ndi mmodzi, maina ao ndi awa; Azirikamu, Bokeru, ndi Ismaele, ndi Seyariya, ndi Obadiya, ndi Hanani; awa ndi ana a Azele.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help