EZEKIELE 16 - Buku Lopatulika Bible 2014

Kusakhulupirika kwa Yerusalemu

1Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

2Ezk. 33.7-9Wobadwa ndi munthu iwe, Dziwitsa Yerusalemu zonyansa zake, nuziti,

3Atero Ambuye Yehova kwa Yerusalemu, Chiyambi chako ndi kubadwa kwako ndiko kudziko la Akanani; atate wako anali Mwamori, ndi mai wako Muhiti.

4Ndipo za kubadwa kwako, tsiku lobadwa iwe sanadule nchofu yako, sanakuyeretse ndi kukusambitsa ndi madzi, sanakuthire mchere konse, kapena kukukulunga m'nsalu ai.

5Panalibe diso linakuchitira chifundo, kukuchitira chimodzi chonse cha izi, kuchitira iwe nsoni; koma unatayidwa kuyere; pakuti ananyansidwa nao moyo wako tsiku la kubadwa kwako.

6Ndipo popita Ine panali iwepo, ndinakuona ulikuvimvinizika m'mwazi mwako. Pamenepo ndinanena ndi iwe m'mwazi wako. Khala ndi moyo, inde ndinati kwa iwe m'mwazi mwako, Khala ndi moyo.

7Eks. 1.7Ndinakuchulukitsa ngati mphundu za kumunda; ndipo unathululuka ndi kukula kufikira wakongola nkhope, mawere ako anamera, ndi tsitsi lako linamera; koma unali wamaliseche ndi wausiwa.

8Rut. 3.9; Yer. 2.2Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakufunda chofunda changa, ndi kuphimba umaliseche wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.

9Ndipo ndinakusambitsa ndi madzi, inde ndinakutsuka kukuchotsera mwazi wako, ndi kukudzoza mafuta.

10Ndinakuvekanso ndi nsalu zopikapika, ndi kukuveka nsapato za chikopa cha katumbu; ndinakuzenenga nsalu yabafuta, ndi kukuphimba ndi nsalu yasilika.

11Gen. 24.22, 30, 47Ndinakukometseranso ndi zokometsera, ndi kuika zigwinjiri m'manja mwako, ndi unyolo m'khosi mwako.

12Gen. 24.22, 30, 47Momwemo ndinaika chipini m'mphuno mwako, ndi maperere m'makutu mwako, ndi korona wokongola pamutu pako.

13Mas. 48.2Ndipo unadzikometsera ndi golide, ndi siliva, ndi chovala chako ndi bafuta ndi silika ndi yopikapika; unadya ufa wosalala, ndi uchi, ndi mafuta; ndipo unali wokongola woposa ndithu, ndipo unapindulapindula kufikira unasanduka ufumu.

14Mali. 2.15Ndi mbiri yako inabuka mwa amitundu chifukwa cha kukongola kwako; pakuti ndiko kwangwiro, mwa ulemerero wanga ndinauika pa iwe, ati Ambuye Yehova.

15 Deut. 32.15 Koma unatama kukongola kwako, ndi kuchita zachigololo potama mbiri yako, ndi kutsanulira zigololo zako pa munthu aliyense wopitapo; unali wake.

162Maf. 23.7Ndipo unatengako zovala zako, ndi kudzimangira misanje ya mawangamawanga, ndi kuchitapo chigololo; zotere sizinayenera kufika kapena kuchitika.

17Unatenganso zokometsera zako zokoma za golide wanga ndi siliva wanga, zimene ndinakupatsa, ndi kudzipangira mafano a amuna, ndi kuchita nao chigololo.

18Unatenganso zovala zako za nsalu yopikapika, ndi kuwaveka nazo, unaikanso mafuta anga ndi chofukiza changa pamaso pao.

19Hos. 2.8Ndi mkate wanga ndinakupatsawo, ufa wosalala, ndi mafuta, ndi uchi, ndinakudyetsazo, unawaikira izi pamaso pao, zichite fungo lokoma; kunatero, ati Ambuye Yehova.

202Maf. 16.3Unatenganso ana ako aamuna ndi aakazi amene unandibalirawo, ndi kuwapereka nsembe awathe. Zigololo zako zidachepa kodi,

21kuti unawapha ana anga ndi kuwapereka, pakuwapititsa pamoto?

22Ndipo pa zonyansa zako zonse ndi zigololo zako sunakumbukira masiku a ubwana wako, muja unakhala wamaliseche ndi wausiwa, wovimvinizika m'mwazi wako.

23Ndipo kudachitika utatha zoipa zako zonse, (tsoka iwe, tsoka, ati Ambuye Yehova)

24unadzimangira nyumba yachimphuli, unadzimangiranso chiunda m'makwalala ali onse.

25Unamanga chiunda chako pa mphambano zilizonse, ndipo unanyansitsa kukongola kwako, ndi kutukula mapazi ako kwa yense wopitako, ndi kuchulukitsa chigololo chako.

26Ezk. 20.7-8Wachitanso chigololo ndi Ejipito oyandikizana nawe, akulu thupi, ndi kuchulukitsa chigololo chako kuutsa mkwiyo wanga.

272Sam. 1.20; Ezk. 16.57Taona tsono, ndakutambasulira dzanja langa, ndi kuchepsa gawo lako la chakudya, ndi kukupereka ku chifuniro cha iwo akudana nawe, kwa ana akazi a Afilisti akuchita manyazi ndi njira yako yoipa.

282Maf. 16.7-18Unachitanso chigololo ndi Aasiriya, pakuti unakhala wosakoledwa, inde unachita chigololo nao, koma sunakoledwa.

29Unachulukitsanso chigololo chako m'dziko la Kanani, mpaka dziko la Ababiloni, koma sunakoledwa nachonso.

30Ha? Mtima wako ngwofooka, ati Ambuye Yehova, pakuchita iwe izi zonse, ndizo ntchito za mkazi wachigololo wouma m'maso.

31Pakumanga nyumba yako yachimphuli pa mphambano zilizonse, ndi pomanga chiunda chako m'makwalala ali onse, sunakhala ngati mkazi wadama waphindu, popeza unapeputsa mphotho.

32Ndiwe mkazi wokwatibwa wochita chigololo, wolandira alendo m'malo mwa mwamuna wake.

33Anthu amaninkha akazi onse achigololo mphatso, koma iwe umaninkha mabwenzi ako onse mphatso zako ndi kuwalipira, kuti akudzere kuchokera kumbali zonse, kuti achite nawe chigololo.

34M'mwemo usiyana konse ndi akazi ena m'chigololo chako; pakuti palibe wokutsata kuchita nawe chigololo; popezanso uwalipira, koma sakupatsa iwe mphotho; potero usiyana nao konse ena.

35Chifukwa chake, wachigololo iwe, tamvera mau a Yehova:

36Ezk. 16.20-21Atero Ambuye Yehova, Popeza ndalama zako zamwazika, nuvundukuka umaliseche wako mwa chigololo chako ndi mabwenzi ako, ndi chifukwa cha mafano onse a zonyansa zako, ndi mwazi wa ana ako umene unawapatsa;

37Mali. 1.8chifukwa chake taona, ndidzasonkhanitsa mabwenzi ako onse amene wakondwera nao, ndi onse unawakonda, pamodzi ndi onse unawada; inde ndidzawasonkhanitsira iwe pozungulira ponse, ndi kuwavundukulira umaliseche wako, kuti aone umaliseche wako wonse.

38Lev. 20.10Ndipo ndidzaweruza mlandu wako, monga aweruza akazi achigololo ndi okhetsa mwazi; ndipo ndidzakutengera mwazi wa ukali ndi wa nsanje.

39Ndidzakuperekanso m'dzanja lao, ndipo adzagwetsa nyumba yako yachimphuli, ndi kugumula ziunda zako, nadzakuvula zovala zako, ndi kulanda zokometsera zako zokongola, nadzakusiya wamaliseche ndi wausiwa.

40Yoh. 8.5, 7Ndipo adzamemezera iwe msonkhano, nadzakuponya miyala, ndi kukupyoza ndi malupanga ao.

412Maf. 25.9Ndipo adzatentha nyumba zako ndi moto, nadzakuweruza pamaso pa akazi ambiri; ndipo ndidzakuleketsa kuchita chigololo, ndipo sudzalipiranso mphotho yachigololo.

42M'mwemo ukali wanga udzakhuta nawe, ndi nsanje yanga idzakuchokera, ndipo ndidzakhala chete wosakwiyanso.

43Ezk. 9.10; 16.22Popeza sunakumbukira masiku a ubwana wako, koma wandivuta nazo zonsezi, chifukwa chake taona, Inenso ndidzakubwezera njira yako pamutu pako, ati Ambuye Yehova; ndipo sudzachita choipa ichi choonjezerapo pa zonyansa zako zonse.

44Taona, aliyense wonena miyambi adzakunenera mwambi uwu, wakuti, Monga make momwemo mwana wake.

45Iwe ndiwe mwana wa mai ako wonyansidwa naye mwamuna wake ndi ana ake, ndipo iwe ndiwe mng'ono wao wa akulu ako akunyansidwa ndi amuna ao ndi ana ao; mai wako ndiye Muhiti, ndi atate wako ndiye Mwamori.

46Deut. 32.32Ndi mkulu wako ndiye Samariya, wokhala kudzanja lako lamanzere, iye ndi ana ake akazi; ndi mng'ono wako wokhala kudzanja lako lamanja ndiye Sodomu ndi ana ake akazi.

47Koma sunayenda m'njira zao, kapena kuchita monga mwa zonyansa zao pang'ono pokha; unawaposa iwo m'kuvunda kwako, m'njira zako zonse.

48Mat. 10.15Pali Ine, ati Ambuye Yehova, Sodomu mng'ono wako sanachita, iye kapena ana ake akazi, monga umo unachitira iwe ndi ana ako akazi.

49Gen. 13.10Taona, mphulupulu ya mng'ono wako Sodomu ndi iye, kudzikuza, kuchuluka kwa chakudya, ndi kupumula kwa mtambasali, anali nako iye ndi ana ake; ndipo sanalimbitse dzanja la wosauka ndi wosowa.

50Gen. 13.13Ndipo anadzikuza, nachita chonyansa pamaso panga; chifukwa chake ndinawachotsa pakuchiona.

51Mat. 12.41-42Ngakhale Samariya sanachite theka la zochimwa zako, koma unachulukitsa zonyansa zako, kuwaposa iwowa, ndi kuika abale ako olungama ndi zonyansa zako zonse unazichita.

52Usenzenso manyazi ako, iwe wakuweruza abale ako mwa zochimwa zako unazichita monyansa koposa iwowa; iwo akuposa iwe m'chilungamo chao, nawenso uchite manyazi nusenze manyazi ako, popeza waika abale ako olungama.

53Deut. 30.1-3Ndipo ndidzabweza undende wao, undende wa Sodomu ndi ana ake, ndi undende wa Samariya ndi ana ake, ndi undende wa andende ako pakati pao;

54kuti usenze manyazi ako, ndi kuti uchite manyazi chifukwa cha zonse unazichita pakuwatonthoza.

55Ndipo abale ako Sodomu ndi ana ake adzabwerera umo unakhalira kale, ndipo Samariya ndi ana ake adzabwerera umo anakhalira kale; ndi iwe ndi ana ako mudzabwerera umo munakhalira kale.

56Ndipo sunakamba za mbale wako Sodomu pakamwa pako tsiku la kudzikuza kwako;

572Maf. 16.5chisanavundukuke choipa chako monga nthawi ya chitonzo cha ana akazi a Aramu, ndi onse akumzungulira iye, ana akazi a Afilisti akupeputsa pozungulira ponse.

58Wasenza choipa chako ndi zonyansa zako, ati Yehova.

59Deut. 29.12-14Pakuti atero Ambuye Yehova, Ndidzachita ndi iwe monga umo unachitira; popeza wapepula lumbiro ndi kuthyola pangano.

60Mas. 106.45; Yer. 32.40Koma ndidzakumbukira Ine pangano langa ndi iwe m'masiku a ubwana wako, ndipo ndidzakhazikitsa pangano losatha nawe.

61Ezk. 20.43Pamenepo udzakumbukira njira zako ndi kuchita manyazi, pakulandira abale ako akulu ndi ang'ono; ndipo ndidzakupatsa awa akhale ana ako akazi, angakhale sali a pangano lako.

62Hos. 2.19-20Pakuti ndidzakhazikitsa pangano langa ndi iwe, ndipo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova;

63Aro. 3.19kuti uzikumbukira ndi kuchita manyazi ndi kusatsegulanso pakamwa pako konse, chifukwa chamanyazi ako, pamene ndikufafanizira zonse unazichita, ati Ambuye Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help