1Wophwanyayo wakwera pamaso pako; sunga linga, yang'anira panjira, limbitsa m'chuuno mwako, limbikitsatu mphamvu yako.
2Pakuti Yehova abwezeranso ukulu wake wa Yakobo ngati ukulu wake wa Israele; pakuti okhuthula anawakhuthula, naipsa nthambi zake za mpesa.
3Yes. 63.2-3Zikopa za amphamvu ake zasanduka zofiira, ngwazi zivala mlangali; magaleta anyezimira ndi chitsulo tsiku la kukonzera kwake, ndi mikondo itinthidwa.
4Magaleta achita mkokomo m'miseu, akankhana m'makwalala; maonekedwe ao akunga miuni, athamanga ngati mphezi.
5Akumbukira omveka ake; akhumudwa m'kupita kwao, afulumira kulinga lake, ndi chotchinjiriza chakonzeka.
6Pa zipata za mitsinje patseguka, ndi chinyumba chasungunuka.
7Chatsimikizika, avulidwa, atengedwa, adzakazi ake alira ngati mau a nkhunda, nadziguguda pachifuwa pao.
8Koma Ninive wakhala chiyambire chake ngati thamanda lamadzi; koma athawa. Imani, Imani! Ati, koma palibe wocheuka.
9Funkhani siliva, funkhani golide; pakuti palibe kutha kwake kwa zosungikazo, kwa chuma cha zipangizo zofunika zilizonse.
10Yes. 13.7-8Ndiye mopanda kanthu mwakemo ndi mwachabe, ndi wopasuka; ndi mtima usungunuka, ndi maondo aombana, ndi m'zuuno zonse muwawa, ndi nkhope zao zatumbuluka.
11Ili kuti ngaka ya mikango, ndi podyera misona ya mikango, kumene mkango, waumuna ndi waukazi, ukayenda ndi mwana wa mkango, kopanda wakuiposa?
12Mkangowo unamwetula zofikira ana ake, nusamira yaikazi yake, nudzaza mapanga ake ndi nyama, ngaka zake ndi zojiwa.
13Ezk. 38.3Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzatentha magaleta ake m'utsi; ndi lupanga lidzadya misona yako ya mkango; ndipo ndidzachotsa zofunkha zako pa dziko lapansi, ndi mau a mithenga yako sadzamvekanso.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.