EZEKIELE 13 - Buku Lopatulika Bible 2014

1Ndipo mau a Yehova anandidzera ine, akuti,

2Yer. 23.16-26Wobadwa ndi munthu iwe, Unenere za aneneri a Israele onenerawo, nuziti nao onenera za m'mtima mwaomwao, Tamverani mau a Yehova.

3Atero Ambuye Yehova, Tsoka aneneri opusawo akutsata mzimu waowao, chinkana sanaone kanthu.

4Aneneri ako, Israele, akhala ngati nkhandwe m'mapululu.

5Mas. 106.23, 30Simunakwera kuima mopasuka, kapena kumanganso linga la nyumba ya Israele, kuima kunkhondo tsiku la Yehova.

6Iwo aona zopanda pake, ndi phenda labodza amene anena, Atero Yehova; koma Yehova sanawatume, nayembekezetsa anthu kuti mauwo adzakhazikika.

7Simunaona masomphenya opanda pake kodi? Simunanena ula wabodza kodi? Pakunena inu, Atero Yehova; chinkana sindinanena?

8Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mwanena zopanda pake, ndi kuona mabodza, chifukwa chake taonani, ndikhala Ine wotsutsana nanu, ati Ambuye Yehova.

9Neh. 7.5Ndi dzanja langa lidzakhala lotsutsana nao aneneri akuona zopanda pake, ndi kupenda za bodza; sadzakhala mu msonkhano wa anthu anga, kapena kulembedwa m'buku lolembedwamo nyumba ya Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

10Yer. 6.14Popeza, inde popeza asokeretsa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, pokhala palibe mtendere; ndipo anthu akamanga linga, aneneriwo alimata ndi dothi losapondeka;

11uziti nao olimata ndi dothi losapondeka, kuti lidzagwa, lidzavumbidwa ndi mvula yaikulu; ndi inu, matalala akulu, mudzagwa; ndi mkuntho udzalithithimula.

12Ndipo taonani, litagwa linga, sadzanena nanu kodi, Lili kuti dothi munalimata nalo?

13Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndidzalithithimula ndi mkuntho m'ukali wanga; ndipo lidzavumbidwa ndi mvula yaikulu mu mkwiyo wanga, ndi matalala akulu adzalitha m'ukali wanga.

14M'mwemo ndidzagumula linga munalimata ndi dothi losapondeka, ndi kuligwetsa pansi; kuti maziko ake agadabuke, ndipo lidzagwa; ndi inu mudzathedwa pakati pake; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

15M'mwemo ndidzakwaniritsa ukali wanga pa lingalo, ndi pa iwo analimata ndi dothi losapondeka, ndipo ndidzati kwa inu, Lingalo palibe, ndi olimata palibe,

16Yer. 6.14ndiwo aneneri a Israele akunenera za Yerusalemu, nauonera masomphenya a mtendere, pamene palibe mtendere, ati Ambuye Yehova.

Mau akutsutsa aneneri akazi onama

17Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, uziika nkhope yako itsutsane nao ana akazi a anthu ako, akunenera za m'mtima mwao, nunenere chowatsutsa,

182Pet. 2.14nuziti, Atero Ambuye Yehova, Tsoka akazi osoka zophimbira mfundo zonse za dzanja, ndi iwo okonza zokuta mitu za misinkhu iliyonse, kuti asake miyoyo! Kodi musaka miyoyo ya anthu anga ndi kudzisungira miyoyo yanu?

19Miy. 28.21Ndipo mundidetsa mwa anthu anga kulandirapo barele wodzala manja, ndi zidutsu za mkate, kuipha miyoyo yosayenera kufa, ndi kusunga miyoyo yosayenera kukhala ndi moyo, ndi kunena mabodza kwa anthu anga omvera bodza.

20Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taonani, nditsutsana nazo zophimbira zanu, zimene musaka nazo miyoyo komweko, kuiuluza; ndipo ndidzazikwatula m'manja mwanu, ndi kuimasula, ndiyo miyoyo muisaka kuiuluza.

21Zokuta mitu zanu zomwe ndidzazing'amba, ndi kulanditsa anthu anga m'manja mwanu; ndipo sadzakhalanso m'mphamvu mwanu kusakidwa; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

22Yer. 23.14Popeza mwamvetsa chisoni ndi mabodza mtima wa wolungama, amene sindinamvetsa chisoni Ine, ndi kumlimbitsa manja woipa, kuti asabwerere kuleka njira yake yoipa, ndi kusungidwa wamoyo;

23Mik. 3.6chifukwa chake simudzaonanso zopanda pake, kapena kupenda; koma ndidzalanditsa anthu anga m'manja mwanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help