LEVITIKO 25 - Buku Lopatulika Bible 2014

Za chaka chopumula dziko

1Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'phiri la Sinai, ndi kuti,

2Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, dzikoli lizisungira Yehova Sabata.

3Zaka zisanu ndi chimodzi ubzale m'munda mwako, ndi zaka zisanu ndi chimodzi udzombole mphesa zako, ndi kucheka zipatso zake;

4koma chaka chachisanu ndi chiwiri chikhale Sabata lakupumula la dziko, Sabata la Yehova; usamabzala m'munda mwako, usamadzombola mipesa yako.

5Zophuka zokha zofikira masika usamazithyola, ndi mphesa za mipesa yako yosadzombola usazicheka; chikhale chaka chopumula dziko.

6Ndipo Sabata la dzikoli likhale kwa inu la chakudya; kwa iwe, ndi mnyamata wako, ndi mdzakazi wako, ndi wolembedwa ntchito yako, ndi mlendo wako wakugonera kwanu;

7ndi ng'ombe zako, ndi nyama zili m'dziko lako; zipatso zake zonse zikhale chakudya chao.

Za chaka choliza lipenga

8Ndipo uziwerengera masabata a zaka asanu ndi awiri, zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawiri; kotero kuti zaka za masabata a zaka asanu ndi awiri, zifikire zaka makumi anai kudza zisanu ndi zinai.

9Pamenepo uzitumizira lipenga lomveka m'mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi la mweziwo; tsiku la chitetezero mutumizire lipenga lifikire m'dziko lanu lonse.

10Ndipo muchipatule chaka cha makumi asanu, ndi kulalikira kwa onse okhala m'dzikomo kuti akhale aufulu; muchiyese chaka choliza lipenga; ndipo mubwerere munthu aliyense ku zakezake, ndipo mubwerere yense ku banja lake.

11Yes. 61.2; Ezk. 46.17Muchiyese chaka cha makumi asanucho choliza lipenga, musamabzala, kapena kucheka zophuka zokha m'mwemo; kapena kucheka mphesa zake za mipesa yosadzombola.

12Popeza ndicho chaka choliza lipenga; muchiyese chopatulika, mudye zipatso zake kunja kwa munda.

13Chaka choliza lipenga ichi mubwerere nonse ku zakezake.

14Ndipo ukagulitsa kanthu kwa mnansi wako, kapena kugula kanthu ka mnansi wako, musamasautsana;

15monga mwa kuwerenga kwake kwa zaka, chitapita choliza lipenga, uzigula kwa mnansi wako, ndi monga mwa kuwerenga kwa zaka za zipatso azigulitsa.

16Monga mwa kuchuluka kwa zaka zake uonjeze mtengo wake, ndi monga mwa kuchepa kwa zaka zake uchepse mtengo wake; pakuti akugulitsa powerenga masiku ake.

17Musamasautsana, koma uope Mulungu wako; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

18M'mwemo muchite malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita; ndipo mudzakhala m'dzikomo okhazikika.

19Dziko lidzaperekanso zipatso zake, ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi kukhalamo okhazikika.

20Ndipo mukadzati, Tidzadyanji chaka chachisanu ndi chiwiri? Taonani, sitidzabzala, sitidzakolola dzinthu;

21pamenepo ndidzauza dalitso langa litsike pa inu chaka chachisanu ndi chimodzi, ndipo chidzapatsa zipatso zofikira zaka zitatu.

22Ndipo mubzale chaka chachisanu ndi chitatu, ndi kudya zipatso zasundwe; kufikira chaka chachisanu ndi chinai, mpaka zitacha zipatso zake mudzadya zasundwe.

Za kuombola dziko ndi nyumba

23 Mas. 85.1; Yow. 3.2 Ndipo asaligulitse dziko chigulitsire; popeza dzikoli ndi langa; pakuti inu ndinu alendo akugonera ndi Ine.

24Potero muzilola liomboledwe dziko lonse muli nalo.

25Mbale wako akasaukira chuma, nakagulitsa chakechake, pamenepo mombolo wake, mbale wake weniweni azidza, naombole chimene mbale wake anagulitsacho.

26Ndipo munthu akasowa mombolo, koma dzanja lake lachionetsa, nachipeza chofikira kuchiombola;

27pamenepo awerenge zaka za kugulitsa kwake, nabwezere wogulayo zotsalirapo nabwerere iye ku dziko lake.

28Koma dzanja lake likapanda kupeza zofikira za kumbwezera, pamenepo chogulitsacho chikhale m'dzanja lake la iye adachigulayo, kufikira chaka choliza lipenga; koma chaka choliza lipenga chituluke, nabwerere iye ku dziko lake.

29Munthu akagulitsa nyumba yogonamo, m'mudzi wa m'linga, aiombole chisanathe chaka choigulitsa; kufikira kutha chaka akhoza kuombola.

30Ndipo akapanda kuiombola kufikira kutha kwake kwa chaka champhumphu, nyumba ili m'mudzi wa m'lingayi idzakhala yake ya iye adaigula yosamchokeranso mwa mibadwo yake; siidzatuluka chaka choliza lipenga.

31Koma nyumba za m'midzi yopanda linga aziyese monga minda ya m'dziko; ziomboledwe, zituluke m'chaka choliza lipenga.

32Kunena za midzi ya Alevi, nyumba za m'midzi yaoyao, Alevi akhoza kuziombola nthawi zonse.

33Ndipo munthu akagula kwa Mlevi, nyumba yogulayo yokhala m'mudzi wakewake, ituluke m'chaka choliza lipenga, popeza nyumba za m'midzi ya Alevi ndizo zaozao mwa ana a Israele.

34Koma dambo la podyera pao siligulika; popeza ndilo laolao kosatha.

35 Mas. 41.1; 1Yoh. 3.17 Ndipo mbale wako akasaukira chuma, ndi dzanja lake lisowa; iwe uzimgwiriziza; akhale nawe monga mlendo wakugonera kwanu.

36Miy. 28.8; Ezk. 18.8Usamambwezetsa phindu, kapena chionjezero; koma uope Mulungu wako; kuti mbale wako akhale nawe.

37Musamampatsa ndalama zako polira phindu, kapena kumpatsa zakudya kuti aonjezerepo pochibwezera.

38Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito, kukupatsani dziko la Kanani, kuti ndikhale Mulungu wanu.

Za mbale wodzigulitsa akhale kapolo

39 Eks. 21.2; Yer. 34.14 Ndipo mbale wako akasaukira chuma, ndi kudzigulitsa kwa iwe; usamamgwiritsa ntchito monga kapolo;

40azikhala nawe ngati wolipidwa ntchito, ngati mlendo wako; akutumikire kufikira chaka choliza lipenga.

41Pamenepo azituluka kukuchokera, iye ndi ana ake omwe, nabwerere ku mbumba yake; abwerere ku dziko laolao la makolo ake.

42Pakuti iwo ndiwo atumiki anga, amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito; asamawagulitsa monga amagulitsa kapolo.

43Aef. 6.9; Akol. 4.1Usamamweruza momzunza; koma uope Mulungu wako.

44Kunena za kapolo wako wamwamuna, kapena wamkazi amene ukhala nao; azikhala a amitundu akuzungulira inu, kwa iwowa muzigula akapolo aamuna ndi aakazi.

45Muwagulenso ana a alendo akukhala mwa inu, a iwowa ndi a mabanja ao akukhala nanu, amene anabadwa m'dziko lanu; ndipo adzakhala anuanu.

46Ndipo muwayese cholowa cha ana anu akudza m'mbuyo, akhale aoao; muwayese akapolo kosatha; koma za abale anu, ana a Israele, musamalamulirana mozunza.

47Ndipo mlendo wakugonera kwanu akalemera chuma, ndi mbale wako wakukhala naye akasauka, nadzigulitsa kwa mlendo wakugonera kwanu, kapena kwa fuko la banja la mlendo;

48atatha kudzigulitsa, aomboledwe; wina wa abale ake amuombole;

49kapena mbale wa atate wake, kapena mwana wa mbale wa atate wake amuombole, kapena mbale wake aliyense wa banja lake amuombole; kapena akalemera chuma yekha adziombole yekha.

50Ndipo awerengere amene anamgulayo kuyambira chaka adadzigulitsa kwa iye kufikira chaka choliza lipenga; ndipo mtengo wake ukhale monga mwa kuwerenga kwa zaka; amuyesere monga masiku a munthu wolipidwa.

51Zikamtsalira zaka zambiri, monga mwa izi abwezere ndalama zakumuombola zochokera ku ndalama zomgulazo.

52Ndipo zikamtsalira zaka pang'ono kufikira chaka choliza lipenga amwerengere; monga mwa zaka zake abwezere mtengo wake wakumuombola.

53Akhale naye monga wolipidwa chaka ndi chaka; asamamlamulira momzunza pamaso pako.

54Ndipo akapanda kumuombola motero, azituluka chaka choliza lipenga, iye ndi ana ake omwe.

55Lev. 25.42; 1Ako. 7.22; Aro. 6.22Pakuti ana a Israele ndi atumiki anga; iwo ndiwo atumiki anga amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help