1 Eks. 15.11-12 Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano;
popeza anachita zodabwitsa:
Dzanja lake lamanja, mkono wake woyera,
zinamchitira chipulumutso.
2 Yes. 52.10 Yehova anawadziwitsira chipulumutso chake;
anaonetsera chilungamo chake pamaso pa amitundu.
3 Mas. 50.3 Anakumbukira chifundo chake ndi chikhulupiriko chake
kunyumba ya Israele;
malekezero onse a dziko lapansi
anaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
4 Mas. 95.1; Yes. 44.23 Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi;
kuwitsani ndi kufuulira mokondwera;
inde, imbirani zomlemekeza.
5Muimbireni Yehova zomlemekeza ndi zeze;
ndi zeze ndi mau a salimo.
6Fuulani pamaso pa Mfumu Yehova,
ndi mbetete ndi liu la lipenga.
7 Mas. 96.10-13 Nyanja ifuule ndi kudzala kwake;
dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhalamo;
8mitsinje iombe manja;
mapiri afuule pamodzi mokondwera.
9Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi;
adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo,
ndipo mitundu ya anthu molunjika.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.