1 Aef. 2.5 Ndipo inu, anakupatsani moyo, pokhala munali akufa ndi zolakwa, ndi zochimwa zanu,
2Akol. 1.21zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera;
3Agal. 5.16amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo;
4Aef. 2.7; Aro. 2.4koma Mulungu, wolemera chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho,
5Aro. 5.6, 8, 10tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (muli opulumutsidwa ndi chisomo),
6Aef. 1.20ndipo anatiukitsa pamodzi, natikhazikitsa pamodzi m'zakumwamba mwa Khristu Yesu;
7Tit. 3.4kuti akaonetsere m'nthawi zilinkudza chuma choposa cha chisomo chake, m'kukoma mtima kwa pa ife mwa Khristu Yesu.
8Yoh. 6.65; Aro. 3.24; 4.16Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu;
9Aro. 3.20, 28chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.
101Ako. 3.9; 2Ako. 5.5, 17Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.
Ayuda ndi amitundu ayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa mtanda wa Khristu11 Akol. 1.21 Momwemo kumbukirani, kuti kale inu amitundu m'thupi, otchedwa kusadulidwa ndi iwo otchedwa mdulidwe m'thupi, umene udachitika ndi manja;
12Yoh. 10.16; Agal. 4.8; Akol. 1.21kuti nthawi ija munali opanda Khristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israele, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi.
13Yes. 57.19; Mac. 2.39Koma tsopano mwa Khristu Yesu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Khristu.
14Mik. 5.5Pakuti Iye ndiye mtendere wathu, amene anachita kuti onse awiri akhale mmodzi, nagumula khoma lakudulitsa pakati,
15Akol. 2.14, 20atachotsa udani m'thupi lake, ndiwo mau a chilamulo cha kutchulako malangizo; kuti alenge awiriwa mwa Iye yekha, akhale munthu mmodzi watsopano, ndi kuchitapo mtendere;
16Akol. 1.20-22ndi kuti akayanjanitse awiriwa ndi Mulungu, m'thupi limodzi mwa mtandawo, atapha nao udaniwo;
17Yes. 57.19; Mac. 2.39ndipo m'mene anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi mtendere kwa iwo apafupi;
18Yoh. 14.6kuti mwa Iye ife tonse awiri tili nao malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi.
19Afi. 3.20Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu;
20Mat. 16.18; 21.42omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Khristu Yesu mwini, mwala wa pangodya;
211Ako. 3.17; Aef. 4.15-16mwa Iye chimango chonse cholumikizika pamodzi bwino, chikula, chikhale Kachisi wopatulika mwa Ambuye;
221Pet. 2.5chimene inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale chokhalamo Mulungu mwa Mzimu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.