MASALIMO 136 - Buku Lopatulika Bible 2014

Mulungu alemekezedwe pa chifundo chake

1 Mas. 106.1 Yamikani Yehova pakuti ndiye wabwino;

pakuti chifundo chake nchosatha.

2Yamikani Mulungu wa milungu;

pakuti chifundo chake nchosatha.

3Yamikani Mbuye wa ambuye;

pakuti chifundo chake nchosatha.

4 Mas. 72.18 Amene yekha achita zodabwitsa zazikulu;

pakuti chifundo chake nchosatha.

5 Yer. 51.15 Amene analenga zakumwamba mwanzeru;

pakuti chifundo chake nchosatha.

6Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi;

pakuti chifundo chake nchosatha.

7 Gen. 1.14, 16 Amene analenga miuni yaikulu;

pakuti chifundo chake nchosatha.

8Dzuwa liweruze usana;

pakuti chifundo chake nchosatha.

9Mwezi ndi nyenyezi ziweruze usiku;

pakuti chifundo chake nchosatha.

10 Eks. 12.29 Iye amene anapandira Aejipito ana ao oyamba;

pakuti chifundo chake nchosatha.

11Natulutsa Israele pakati pao;

pakuti chifundo chake nchosatha.

12Ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka;

pakuti chifundo chake nchosatha.

13 Eks. 14.21-22 Amene anagawa magawo Nyanja Yofiira;

pakuti chifundo chake nchosatha.

14Napititsa Israele pakati pake;

pakuti chifundo chake nchosatha.

15 Eks. 14.27 Nakhuthula Farao ndi khamu lake m'Nyanja Yofiira:

pakuti chifundo chake nchosatha.

16 Eks. 15.22 Amene anatsogolera anthu ake m'chipululu;

pakuti chifundo chake nchosatha.

17 Deut. 29.7 Amene anapanda mafumu akulu;

pakuti chifundo chake nchosatha.

18Ndipo anawapha mafumu omveka;

pakuti chifundo chake nchosatha.

19Sihoni mfumu ya Aamori;

pakuti chifundo chake nchosatha.

20Ndi Ogi mfumu ya Basani;

pakuti chifundo chake nchosatha.

21 Yos. 12 Ndipo anapereka dziko lao likhale chosiyira;

pakuti chifundo chake nchosatha.

22Chosiyira cha kwa Israele mtumiki wake;

pakuti chifundo chake nchosatha.

23Amene anatikumbukira popepuka ife;

pakuti chifundo chake nchosatha.

24Natikwatula kwa otisautsa;

pakuti chifundo chake nchosatha.

25 Mas. 104.27 Ndiye wakupatsa nyama zonse chakudya;

pakuti chifundo chake nchosatha.

26Yamikani Mulungu wa kumwamba;

pakuti chifundo chake nchosatha.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help