1 AKORINTO 8 - Buku Lopatulika Bible 2014

Kunena za kudya nyama yoperekedwa nsembe kwa mafano

1 Mac. 15.20, 29; 1Ako. 13.4 Koma za zoperekedwa nsembe kwa mafano: Tidziwa kuti tili nacho chidziwitso tonse. Chidziwitso chitukumula, koma chikondi chimangirira.

21Ako. 13.9, 12Ngati wina ayesa kuti adziwa kanthu sanayambe kudziwa monga ayenera kudziwa.

3Nah. 1.7; 2Tim. 2.19Koma ngati wina akonda Mulungu, yemweyu adziwika ndi Iye.

4Deut. 4.39Tsono kunena za kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano silili kanthu pa dziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma mmodzi.

5Pakuti ngakhalenso iliko yoti yonenedwa milungu, kapena m'mwamba, kapena pa dziko lapansi, monga iliko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri;

6Mala. 2.10; Yoh. 13.13; Akol. 1.16koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Khristu, amene zinthu zonse zili mwa Iye, ndi ife mwa Iye.

71Ako. 10.28-29Komatu chidziwitso sichili mwa onse; koma ena, ozolowera fano kufikira tsopano, adyako monga yoperekedwa nsembe kwa fano; ndipo chikumbu mtima chao, popeza nchofooka, chidetsedwa.

8Aro. 14.17Koma chakudya sichitivomerezetsa kwa Mulungu; kapena ngati sitidya sitisowa; kapena ngati tidya tilibe kupindulako.

9Aro. 14.13-14; Agal. 5.13Koma yang'anirani kuti ulamuliro wanu umene ungakhale chokhumudwitsa ofookawo.

101Ako. 10.28, 32Pakuti wina akaona iwe amene uli nacho chidziwitso, ulikukhala pachakudya m'Kachisi wa fano, kodi chikumbu mtima chake, popeza ali wofooka, sichidzalimbika kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano?

11Aro. 14.15, 20Pakuti mwa chidziwitso chako wofookayo atayika, ndiye mbale amene Khristu anamfera.

12Mat. 25.40, 45Koma pakuchimwira abale, ndi kulasa chikumbu mtima chao chofooka, muchimwira kotero Khristu.

13Aro. 14.21Chifukwa chake, ngati chakudya chikhumudwitsa mbale wanga, sindidzadya nyama kunthawi yonse, kuti ndingakhumudwitse mbale wanga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help