1 Yer. 51.13; Chiv. 18.16 Ndipo anadza mmodzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nalankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa chitsutso cha mkazi wachigololo wamkulu, wakukhala pa madzi ambiri,
2Chiv. 18.3amene mafumu a dziko anachita chigololo naye, ndipo iwo akukhala padziko analedzera ndi vinyo wa chigololo chake.
3Chiv. 12.3Ndipo ananditenga kunka nane kuchipululu, mu Mzimu; ndipo ndinaona mkazi alinkukhala pachilombo chofiira, chodzala ndi maina a mwano, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.
4Chiv. 18.12-16Ndipo mkazi anavala chibakuwa, ndi mlangali, nakometsedwa ndi golide, ndi miyala ya mtengo wake, ndi ngale; nakhala nacho m'dzanja lake chikho chagolide chodzala ndi zonyansitsa, ndi zodetsa za chigololo chake,
5Chiv. 18.9; 19.2ndipo pamphumi pake padalembedwa dzina, CHINSINSI, BABILONI WAUKULU, AMAI WA ACHIGOLOLO NDI WA ZONYANSITSA ZA DZIKO.
6Chiv. 16.6Ndipo ndinaona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu; ndipo ndinazizwa pakumuona iye ndi kuzizwa kwakukulu.
7Ndipo mngelo anati kwa ine, Uzizwa chifukwa ninji? Ine ndidzakuuza iwe chinsinsi cha mkazi, ndi cha chilombo chakumbereka iye, chokhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.
8Chiv. 11.7; 13.8Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m'chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako.
9Pano pali mtima wakukhala nayo nzeru. Mitu isanu ndi iwiri ndiyo mapiri asanu ndi awiri amene mkazi akhalapo;
10ndipo ali mafumu asanu ndi awiri asanu adagwa, imodzi iliko, yinayo siinadze; ndipo pamene ifika iyenera iyo kukhala kanthawi.
11Ndipo chilombo chinalicho, ndi kulibe, icho chomwe ndicho chachisanu ndi chitatu, ndipo chili mwa zisanu ndi ziwirizo, nichimuka kuchitayiko.
12Dan. 7.20; Zek. 1.18-21Ndipo nyanga khumi udaziona ndiwo mafumu khumi, amene sanalandire ufumu; koma alandira ulamuliro ngati mafumu, ora limodzi, pamodzi ndi chilombo.
13Iwo ali nao mtima umodzi, ndipo apereka mphamvu ndi ulamuliro wao kwa chilombo.
14Deut. 10.17; 1Tim. 6.15; Chiv. 2.10; 16.14; 19.19-21Iwo adzachita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawalaka, chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika.
15Chiv. 17.1Ndipo anena ndi ine, Madziwo udawaona uko akhalako mkazi wachigololoyo ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe.
16Yer. 50.41-42Ndipo nyanga khumi udaziona, ndi chilombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, nizidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yake, nizidzampsereza ndi moto.
172Ate. 2.11Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwao kuchita za m'mtima mwake, ndi kuchita cha mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa chilombo, kufikira akwaniridwa mau a Mulungu.
18Chiv. 16.19Ndipo mkaziyo unamuona, ndiye mudzi waukulu, wakuchita ufumu pa mafumu a dziko.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.