1 Mas. 6.1 Yehova, musandidzudzule ndi mkwiyo wanu,
ndipo musandilange moopsa m'mtima mwanu.
2 Mas. 32.4 Pakuti mivi yanu yandilowa,
ndi dzanja lanu landigwera.
3Mumnofu mwanga mulibe chamoyo chifukwa cha ukali wanu;
ndipo m'mafupa anga simuzizira, chifukwa cha cholakwa changa.
4 Ezr. 9.6 Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga;
ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera.
5Mabala anga anunkha, adaola,
chifukwa cha kupusa kwanga.
6Ndapindika, ndawerama kwakukulu;
ndimayenda woliralira tsiku lonse.
7Pakuti m'chuuno mwanga mutentha kwambiri;
palibe pamoyo m'mnofu mwanga.
8Ndafooka ine, ndipo ndachinjizidwa,
ndabangula chifukwa cha kumyuka mtima wanga.
9Ambuye, chikhumbo changa chonse chili pamaso panu;
ndipo kubuula kwanga sikubisika kwa Inu.
10 Mas. 88.9 Mtima wanga ugundagunda, mphamvu yanga yachoka,
ndipo kuunika kwa maso anga, ndi iko komwe kwandichokera.
11 Mas. 88.18 Ondikonda ndi anzanga apewa mliri wanga;
ndipo anansi anga aima patali.
12 2Sam. 17.1-3 Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga;
ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga,
nalingirira zonyenga tsiku lonse.
13 Mas. 39.2, 9 Koma ine, monga gonthi, sindimva;
ndipo monga munthu wosalankhula,
sinditsegula pakamwa panga.
14Inde ndikunga munthu wosamva,
ndipo m'kamwa mwanga mulibe makani.
15 2Sam. 16.12 Pakuti ndikuyembekezani Inu, Yehova;
Inu mudzayankha, Ambuye Mulungu wanga.
16Pakuti ndinati, Asakondwerere ine;
pakuterereka phazi langa, asadzikuze pa ine.
17Ndafikana potsimphina,
ndipo chisoni changa chili pamaso panga chikhalire.
18 Mas. 32.5; Miy. 28.13; 2Ako. 7.9-10 Pakuti ndidzafotokozera mphulupulu yanga;
nditenga nkhawa chifukwa cha tchimo langa.
19Koma adani anga ali ndi moyo, nakhala ndi mphamvu,
ndipo akundida kopanda chifukwa achuluka.
20 Mas. 35.12 Ndipo iwo akubwezera choipa pa chabwino
atsutsana nane, popeza nditsata chabwino.
21 Mas. 35.22 Musanditaye, Yehova,
Mulungu wanga, musakhale kutali ndi ine.
22 Mas. 40.13 Fulumirani kundithandiza,
Ambuye, chipulumutso changa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.