1 Mas. 50.14 M'Ziyoni akulemekezani Inu mwachete, Mulungu,
adzakuchitirani Inu chowindachi.
2 Yes. 66.23 Wakumva pemphero Inu,
zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.
3 Mas. 51.2; Yes. 6.7; Aheb. 9.14 Mphulupulu zinandilaka;
koma mudzafafaniza zolakwa zathu.
4 Mas. 33.12; 36.8 Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa,
akhale m'mabwalo anu.
Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu,
za m'malo oyera a Kachisi wanu.
5 Mas. 22.27 Mudzatiyankha nazo zoopsa m'chilungamo,
Mulungu wa chipulumutso chathu;
ndinu chikhulupiriko cha malekezero onse a dziko lapansi,
ndi cha iwo okhala kutali kunyanja.
6Ndinu amene mukhazikitsa mapiri ndi mphamvu yanu;
pozingidwa nacho chilimbiko.
7 Yes. 17.12-13; Mat. 8.26 Amene atontholetsa kukuntha kwa nyanja,
kukuntha kwa mafunde ake,
ndi phokoso la mitundu ya anthu.
8Ndipo iwo akukhala kumalekezero adzachita mantha
chifukwa cha zizindikiro zanu;
mukondweretsa apo patulukira dzuwa, ndi apo lilowera.
9 Mas. 46.4 Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira,
mulilemeza kwambiri;
mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi,
muwameretsera tirigu m'mene munakonzera nthaka.
10Mukhutitsa nthaka yake yolima;
mufafaniza nthumbira zake;
muiolowetsa ndi mvumbi;
mudalitsa mmera wake.
11Muveka chakachi ndi ukoma wanu;
ndipo mabande anu akukha zakucha.
12Akukha pa mabusa a m'chipululu;
ndipo mapiri azingika nacho chimwemwe.
13 Yes. 55.12 Podyetsa mpodzaza ndi zoweta;
ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu;
zifuula mokondwera, inde ziimbira.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.