1
17Khwalala la oongoka mtima ndilo lakuti asiye zoipa;
wosunga njira yake atchinjiriza moyo wake.
18Kunyada kutsogolera kuonongeka;
mtima wodzikuza ndi kutsogolera kuphunthwa.
19 Yes. 57.15 Kufatsa mtima ndi osauka
kuposa kugawana zofunkha ndi onyada.
20 Mas. 2.12; Yes. 30.18 Wolabadira mau adzapeza bwino;
ndipo wokhulupirira Yehova adala.
21Wanzeru mtima adzatchedwa wochenjera;
ndipo kukoma kwa milomo kuonjezera kuphunzira.
22Nzeru ndi kasupe wa moyo kwa mwini wake;
koma mwambo wa zitsiru ndi utsiru.
23 Mat. 12.34-35 Mtima wa wanzeru uchenjeza m'kamwa mwake,
nuphunzitsanso milomo yake.
24Mau okoma ndiwo chisa cha uchi,
otsekemera m'moyo ndi olamitsa mafupa.
25Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka,
koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.
26Wantchito adzigwirira yekha ntchito;
pakuti m'kamwa mwake mumfulumiza.
27Munthu wopanda pake akonzeratu zoipa;
ndipo m'milomo mwake muli moto wopsereza.
28Munthu wokhota amautsa makani;
kazitape afetsa ubwenzi.
29Munthu wa chiwawa akopa mnzake,
namuyendetsa m'njira yosakhala bwino.
30Wotsinzina ndiye aganizira zokhota;
wosunama afikitsa zoipa.
31 Miy. 20.29 Imvi ndiyo korona wa ulemu,
idzapezedwa m'njira ya chilungamo.
32Wosakwiya msanga aposa wamphamvu;
wolamulira mtima wake naposa wolanda mudzi.
33 Mac. 1.26 Maere aponyedwa pamfunga;
koma ndiye Yehova alongosola zonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.