1 Mas. 127.1; Aef. 2.20-22 Nzeru yamanga nyumba yake,
yasema zoimiritsa zake zisanu ndi ziwiri;
2yaphera nyama yake, nisanganiza vinyo wake,
nilongosolanso pa gome lake.
3Yatuma anamwali ake, iitana
pa misanje ya m'mudzi.
4 Mat. 11.25 Wazibwana yense apatukire kuno;
iti kwa yense wosowa nzeru,
5 Yoh. 6.27 Tiyeni, idyani chakudya changa;
nimumwe vinyo wanga ndamsanganiza.
6Lekani, achibwana inu, nimukhale ndi moyo;
nimuyende m'njira ya nzeru.
7Woweruza munthu wonyoza adzichititsa yekha manyazi;
yemwe adzudzula wochimwa angodetsa mbiri yakeyake.
8 Mas. 141.5; Mat. 7.6 Usadzudzule wonyoza kuti angakude;
dzudzula wanzeru adzakukonda.
9 Mat. 13.12 Ukachenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yake;
ukaphunzitsa wolungama adzaonjezera kuphunzira.
10 Mas. 111.10 Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova;
kudziwa Woyerayo ndiko luntha.
11Pakuti mwa ine masiku ako adzachuluka,
zaka za moyo wako zidzaonjezedwa.
12 Yob. 35.6-7 Ukakhala wanzeru, si yakoyako nzeruyo?
Ndipo ukanyoza udzasauka wekha.
13Utsiru umalongolola,
ngwa chibwana osadziwa kanthu.
14Ukhala pa khomo la nyumba yake,
pampando pa misanje ya m'mudzi,
15kuti uitane akupita panjira,
amene angonkabe m'kuyenda kwao,
16wachibwana ndani? Apatukire kuno.
Ati kwa yense wopanda nzeru,
17 Miy. 20.17 madzi akuba atsekemera,
ndi chakudya chobisika chikoma.
18Ndipo mwamunayo sadziwa kuti akufa ali konko;
omwe achezetsa utsiru ali m'manda akuya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.