1 Gen. 27.34; 2Sam. 1.11 Koma podziwa Mordekai zonse zidachitikazi, Mordekai anang'amba zovala zake, navala chiguduli ndi mapulusa, natuluka pakati pa mudzi, nafuula, nalira kulira kwakukulu ndi kowawa,
2nafika popenyana ndi chipata cha mfumu; popeza sanathe munthu kulowa kuchipata cha mfumu wovala chiguduli.
3Ndi m'maiko monse, paliponse anafikapo mau a mfumu ndi lamulo lake, panali maliro akulu mwa Ayuda, ndi kusala, ndi kulira misozi, ndi kubuma; nagona m'chiguduli ndi mapulusa ambiri.
4Ndipo anamwali a Estere ndi adindo ake anadza, namuuza; ndi mkazi wamkulu anawawidwa mtima kwambiri, natumiza chovala aveke Mordekai, ndi kumchotsera chiguduli chake; koma sanachilandira.
5Pamenepo Estere anaitana Hataki mdindo wina wa mfumu, amene idamuika amtumikire, namuuza amuke kwa Mordekai, kuti adziwe ichi nchiyani ndi chifukwa chake ninji.
6Natuluka Hataki kunka kwa Mordekai kukhwalala la mudzi linali popenyana ndi chipata cha mfumu.
7Ndipo Mordekai anamfotokozera zonse zidamgwera, ndi mtengo wake wa ndalama adati Hamani adzapereka m'nyumba ya chuma cha mfumu pa Ayuda, kuwaononga.
8Est. 3.14-15Anampatsanso chitsanzo cha lamulo lolembedwa adalibukitsa m'Susa, kuwaononga, achionetse kwa Estere, ndi kumfotokozera, ndi kumlangiza alowe kwa mfumu, kumpembedza, ndi kupempherera anthu ake kwa iye.
9Nadza Hataki, namuuza Estere mau a Mordekai.
10Pamenepo Estere ananena ndi Hataki, namtuma akauze Mordekai, ndi kuti,
11Est. 5.1-2; 8.4Akapolo onse a mfumu ndi anthu a m'maiko a mfumu adziwa kuti aliyense, ngakhale wamwamuna kapena wamkazi, akalowa kwa mfumu kubwalo la m'katimo wosaitanidwa, lamulo la pa iye ndi limodzi, ndilo kuti amuphe, akapanda mfumu kumloza ndi ndodo yachifumu yagolide kuti akhale ndi moyo; koma ine sanandiitane ndilowe kwa mfumu masiku awa makumi atatu.
12Ndipo anamuuza Mordekai mau a Estere.
13Koma Mordekai anawauza ambwezere mau Estere, kuti, Usamayesa m'mtima mwako kuti udzapulumuka m'nyumba ya mfumu koposa Ayuda onse ena.
14Pakuti ukakhala chete konse tsopano lino, chithandizo ndi chipulumutso kwa Ayuda zidzafuma kwina; koma iwe ndi nyumba ya atate wako mudzaonongeka; ndipo kaya, kapena walowera ufumu chifukwa cha nyengo yonga iyi.
15Pamenepo Estere anati ambwezere mau Mordekai,
16Gen. 43.14Muka, sonkhanitsa Ayuda onse opezeka m'Susa, nimundisalire, osadya osamwa masiku atatu, usiku ndi usana, ine ndemwe ndi anamwali anga tidzasala momwemo, ndipo motero ndidzalowa kwa mfumu, ndiko kosalingana ndi lamulo; ndikaonongeka tsono ndionongeke.
17Napita Mordekai, nachita monga mwa zonse adamlamulira Estere.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.