MASALIMO 91 - Buku Lopatulika Bible 2014

Mulungu asungadi wodzipereka kwa Iye

1 Mas. 27.5; 17.8 Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba

adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.

2 Mas. 142.5 Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa;

Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.

3 Mas. 124.7 Pakuti adzakuonjola kumsampha wa msodzi,

kumliri wosakaza.

4 Mas. 61.4 Adzakufungatira ndi nthenga zake,

ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ake;

choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza.

5 Miy. 3.23-24 Sudzaopa choopsa cha usiku,

kapena muvi wopita usana;

6kapena mliri woyenda mumdima,

kapena chionongeko chakuthera usana.

7Pambali pako padzagwa chikwi,

ndi zikwi khumi pa dzanja lamanja lako;

sichidzakuyandikiza iwe.

8 Mala. 1.4-5 Koma udzapenya ndi maso ako,

nudzaona kubwezera chilango oipa.

9 Mas. 71.3 Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo panga!

Udaika Wam'mwambamwamba chokhalamo chako;

10 Miy. 12.21 palibe choipa chidzakugwera,

ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako.

11 Mat. 4.6 Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe,

akusunge m'njira zako zonse.

12Adzakunyamula pa manja ao,

ungagunde phazi lako pamwala.

13Udzaponda mkango ndi mphiri;

udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka.

14 Mas. 9.10 Popeza andikondadi ndidzampulumutsa;

ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.

15 Mas. 27.4 Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha;

kunsautso ndidzakhala naye pamodzi;

ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.

16Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri,

ndi kumuonetsera chipulumutso changa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help