1 AKORINTO 10 - Buku Lopatulika Bible 2014

Tisayese dala Mulungu monga Israele

1 Eks. 13.21-22; 14.22 Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse;

2nabatizidwa onse kwa Mose, mumtambo, ndi m'nyanja,

3Eks. 16.15-35nadya onse chakudya chauzimu chimodzimodzi;

4Eks. 17.6namwa onse chakumwa chauzimu chimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiye Khristu.

5Num. 14.29, 32, 35Koma ochuluka a iwo Mulungu sanakondwera nao; pakuti anamwazika m'chipululu.

6Koma zinthu izi zinachitika, zikhale zotichenjeza ife, kuti tisalakalake zoipa ife, monganso iwowo analakalaka.

7Eks. 32.6Kapena musakhale opembedza mafano, monga ena a iwo, monga kwalembedwa, Anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kusewera.

8Num. 25.1-9Kapena tisachite dama monga ena a iwo anachita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi awiri ndi zitatu.

9Num. 21.5-9Kapena tisayese Ambuye, monga ena a iwo anayesa, naonongeka ndi njoka zija.

10Num. 14.2-29Kapena musadandaula, monga ena a iwo anadandaula, naonongeka ndi woonongayo.

11Aro. 15.4Koma izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife.

12Aro. 11.20Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang'anire kuti angagwe.

132Pet. 2.9Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

Za kupembedza mafano, za kuyanjana ndi ziwanda

14Chifukwa chake, okondedwa anga, thawani kupembedza mafano.

15Ndinena monga kwa anzeru; lingirirani inu chimene ndinena.

16Mat. 26.26-28Chikho cha dalitso chimene tidalitsa, sichili chiyanjano cha mwazi wa Khristu kodi? Mkate umene tinyema suli chiyanjano cha thupi la Khristu kodi?

17Aro. 12.5Pakuti mkate ndiwo umodzi, chotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse titengako kumkate umodzi.

18Lev. 7.15Tapenyani Israele monga mwa thupi; kodi iwo akudya nsembezo alibe chiyanjano ndi guwa la nsembe?

191Ako. 8.4Ndinena chiyani tsono? Kuti choperekedwa nsembe kwa mafano chili kanthu? Kapena kuti fano lili kanthu kodi?

20Deut. 32.17Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda osati kwa Mulungu; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda.

212Ako. 6.15-16Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda.

22Deut. 32.21Kapena kodi tichititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa Iye?

Mkhristu ndiye mfulu koma wosamalira ena

23 1Ako. 6.12 Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.

24Aro. 15.1-2Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.

251Tim. 4.4Chonse chogulitsidwa pa msika wa nyama, mudye, osafunsa kanthu chifukwa cha chikumbu mtima;

26Mas. 24.1pakuti dziko lapansi lili la Ambuye, ndi kudzala kwake.

27Luk. 10.7Ngati wina wa osakhulupirira akuitanani, ndipo mufuna kupita; mudye chomwe chiikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, chifukwa cha chikumbu mtima.

281Ako. 8.10Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, chifukwa cha iyeyo wakuuza, ndi chifukwa cha chikumbu mtima.

29Aro. 14.16Ndinena chikumbu mtima, si cha iwe mwini, koma cha winayo; pakuti ufulu wanga uyesedwa ninji ndi chikumbu mtima cha wina?

30Ngati ine ndilandirako mwachisomo, ndinenezedwa bwanji chifukwa cha ichi chimene ndiyamikapo?

31Akol. 3.17Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.

32Aro. 14.13Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Agriki, kapena Mpingo wa Mulungu;

33Aro. 15.2monga inenso ndikondweretsa onse m'zinthu zonse, wosafuna chipindulo changa, koma cha unyunjiwo, kuti apulumutsidwe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help