MIYAMBO 17 - Buku Lopatulika Bible 2014

1 Miy. 15.17 Nyenyeswa youma, pokhala mtendere,

iposa nyumba yodzala nyama yansembe, pali makangano.

2Kapolo wochita mwanzeru

adzalamulira mwana wochititsa manyazi,

nadzagawana nao abale cholowa.

3 Yer. 17.10; Mala. 3.3 Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golide ali ndi ng'anjo;

koma Yehova ayesa mitima.

4Wochimwa amasamalira milomo yolakwa;

wonama amvera lilime losakaza.

5 Miy. 14.31; Oba. 1.12 Wochitira chiphwete aumphawi atonza Mlengi;

wokondwera ndi tsoka sadzapulumuka chilango.

6 Mas. 127.3; 128.6 Zidzukulu ndizo korona wa okalamba;

ndipo ulemerero wa ana ndiwo atate ao.

7Mlomo wangwiro suyenera chitsiru;

ngakhale mlomo wonama suyenera kalonga ndi pang'ono ponse.

8Wolandira chokometsera mlandu achiyesa ngale;

paliponse popita iye achenjera.

9 Miy. 10.12 Wobisa cholakwa afunitsa chikondano;

koma wobwerezabwereza mau afetsa ubwenzi.

10Chidzudzulo chilowa m'kati mwa wozindikira,

kopambana ndi kukwapula wopusa kwambiri.

11Woipa amafuna kupanduka kokha;

koma adzamtumizira mthenga wankhanza.

12 Hos. 13.8 Kukomana ndi chitsiru m'kupusa kwake

kuopsa koposa chilombo chochichotsera anake.

13 Gen. 40.23 Wobwezera zabwino zoipa,

zoipa sizidzamchokera kwao.

14 1Ate. 4.11 Chiyambi cha ndeu chifanana ndi kutsegulira madzi;

tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.

15 Eks. 23.7 Wokometsa mlandu wa wamphulupulu,

ndi wotsutsa wolungama,

onse awiriwa amnyansa Yehova.

16Kodi bwanji mtengo wogulira nzeru uli m'dzanja la chitsiru,

popeza wopusa alibe mtima?

17 Rut. 1.16; Yob. 6.14 Bwenzi limakonda nthawi zonse;

ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.

18Munthu wosowa nzeru apangana kulipirira wina,

napereka chikole pamaso pa mnzake.

19Wokonda ndeu akonda kulakwa;

ndipo wotalikitsa khomo lake afunafuna kuonongeka.

20 Yak. 3.8 Wokhota mtima sadzapeza bwino;

ndipo mwini lilime lokhota adzagwa m'zoipa.

21Wobala chitsiru adzichititsa chisoni;

ndipo atate wa wopusa sakondwa.

22 Miy. 15.13-15 Mtima wosekerera uchiritsa bwino;

koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.

23 Eks. 23.8 Munthu woipa alandira chokometsera mlandu chotulutsa m'mfunga,

kuti apatukitse mayendedwe a chiweruzo.

24 Mlal. 8.1 Nzeru ili pamaso pa wozindikira;

koma maso a wopusa ali m'malekezero a dziko.

25Mwana wopusa achititsa atate wake chisoni,

namvetsa zowawa amake wombala.

26Kulipiritsa wolungama sikuli kwabwino,

ngakhale kukwapula akulu chifukwa aongoka mtima.

27 Yak. 1.19 Wopanda chikamwakamwa apambana kudziwa;

ndipo wofatsa mtima ali wanzeru.

28 Yob. 13.5 Ngakhale chitsiru chikatonthola achiyesa chanzeru;

posunama ali wochenjera.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help