YESAYA 44 - Buku Lopatulika Bible 2014

Mulungu ndi wamkulukulu, mafano ndi achabe

1 Yer. 30.10 Koma tsopano, imva Yakobo, mtumiki wanga, ndi Israele, amene ndakusankha;

2atero Yehova, amene anakutenga iwe, nakuumba kuchokera m'mimba, amene adzathangata iwe. Usaope Yakobo, mtumiki wanga ndi iwe, Yesuruni, amene ndakusankha iwe.

3Yes. 35.6-7; Yow. 2.28; Yoh. 7.38; Mac. 2.18Pakuti ndidzathira madzi pa dziko limene lilibe madzi, ndi mitsinje pa nthaka youma; ndidzathira mzimu wanga pa mbeu yako, ndi mdalitso wanga pa obadwa ako;

4Mas. 1.3ndipo iwo adzaphuka pakati pa udzu, ngati msondodzi m'mphepete mwa madzi.

5Wina adzati, Ine ndili wa Yehova; ndi wina adzadzitcha yekha ndi dzina la Yakobo, ndipo wina adzalemba ndi dzanja lake, Ndine wa Yehova, ndi kudzitcha yekha ndi mfunda wa Israele.

6 Yes. 41.4; 43.1, 14 Atero Yehova, mfumu ya Israele ndi Mombolo wake, Yehova wa makamu, Ine ndili woyamba ndi womaliza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu.

7Ndipo ndani adzaitana monga Ine, ndi kulalikira ichi ndi kundilongosolera ichi, chikhazikitsire Ine anthu akale? Milunguyo iwadziwitse zomwe zilinkudza, ndi za m'tsogolo.

8Deut. 4.35, 39; Yes. 43.10Musaope inu, musakhale ndi mantha; kodi ndinanena kwa iwe zakale, ndi kuzionetsa zimenezo, ndipo inu ndinu mboni zanga. Kodi popanda Ine aliponso Mulungu? Iai, palibe thanthwe; sindidziwa lililonse.

9Yes. 41.29Omwe apanga fano losema onsewo asokonezeka; ndipo zokondweretsa zao sadzapindula nazo kanthu; ndipo mboni zao siziona, kapena kudziwa; kuti akhale ndi manyazi.

10Ndani wapanga mulungu, kapena kusungunula fano losema losapindula kanthu?

11Mas. 97.7Taonani anzake onse adzakhala ndi manyazi, ndi amisiri ake ndi anthu; asonkhane onse pamodzi, aimirire; adzaopa, iwo onse adzakhala ndi manyazi.

12Yes. 40.19Wachipala achita zake ndi nsompho, nagwira ntchito ndi makala, nafanizira fanolo ndi nyundo, nagwira ntchito yake ndi mkono wake wamphamvu; inde, ali ndi njala, ndipo mphamvu zake zilephera; iye samwa madzi, nalefuka.

13Mmisiri wa mitengo atambalitsa chingwe; nalilemba ndi cholembera, nalikonza ndi ncherero, nalilemba ndi zolinganizira, nalifanizira monga maonekedwe a munthu, monga munthu wokongola, kuti likhale m'nyumba.

14Iye adzidulira yekha mikungudza, natenga mtengo wambawa, ndi wathundu, ndi kudzisankhira yekha wina wa mitengo ya nkhalango; naoka mtengo wamlombwa, mvula niukulitsa.

15Ndipo udzakhala kuti munthu autenthe; iye natengako, nauotha moto; inde auyatsa, naocha mkate; inde, apanga mulungu, naulambira, naupanga fano losema, naligwadira.

16Iye atenthako mbali ina pamoto; ndi mbali yinayo adya nyama; akazinga zokazinga nakhuta, inde, aotha moto, nati, Ha, ndakongonoka, ndauona moto.

17Ndipo chotsalacho apanga mulungu, ngakhale fano lake losema; iye aligwadira, nalipembedza, nalipemphera nati, Ndipulumutse ine, chifukwa kuti ndinu mulungu wanga.

182Ate. 2.11Iwo sadziwa, kapena kuzindikira, chifukwa pamaso mwao papakidwa thope, kuti sangaone, ndi m'mitima mwako kuti sangadziwitse.

19Palibe wina wokumbukira, kapena kudziwa, kapena kuzindikira, ndi kuti, Ndatentha mbali ina pamoto, inde ndaochanso mkate pamakala pake, ndakazinga nyama ndi kuidya; kodi ndichipange chotsala chake, chikhale chonyansa? Ndidzagwadira kodi tsinde la mtengo?

20Aro. 1.21Iye adya phulusa; mtima wodzinyenga wampambutsa, kuti iye sangapulumutse moyo wake, pena kunena, Kodi simuli kunama m'dzanja langa lamanja?

Mulungu Mpulumutsi wa Israele

21 Yes. 44.1-2 Kumbukirani zinthu izi, Yakobo; ndi Israele, pakuti iwe ndiwe mtumiki wanga; ndakuumba, iwe ndiwe mtumiki wanga, Israele, sindidzakuiwala.

22Yes. 43.25; 44.6; 48.20; 1Ako. 6.20Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.

23Yes. 42.10Imbani m'mwamba inu, pakuti Yehova wachichita icho; kuwani inu, mbali za pansi pa dziko; imbani mapiri inu; nkhalango iwe, ndi mitengo yonse m'menemo; chifukwa kuti Yehova wapulumutsa Yakobo, ndipo adzadzilemekezetsa yekha mwa Israele.

24 Yes. 44.2, 6 Atero Yehova, Mombolo wako, ndi Iye amene anakuumba iwe m'mimba, Ine ndine Yehova, amene ndipanga zinthu zonse, ndi kufunyulula ndekha zakumwamba, ndi kuyala dziko lapansi; ndani ali ndi Ine?

25Yer. 50.36; 1Ako. 1.20Ndine amene nditsutsa zizindikiro za matukutuku, ndi kuchititsa misala oombeza ula; ndi kubwezera m'mbuyo anthu anzeru, ndi kupusitsa nzeru zao:

26Zek. 1.6Ndine amene ndilimbitsa mau a mtumiki wanga, kuchita uphungu wa amithenga anga; ndi kunena za Yerusalemu, Adzakhalamo anthu; ndi za midzi ya Yuda; Idzamangidwa; ndipo ndidzautsa malo abwinja ake.

27Yer. 50.38Ndine amene nditi kwa nyanja yakuya, Iphwa, ndipo ndidzaumitsa nyanja zako;

282Mbi. 36.22-23; Ezr. 1.1-3ndi kunena za Kirusi, Iye ndiye mbusa wanga, ndipo adzachita zofuna zanga zonse; ndi kunena za Yerusalemu, Adzamangidwa; ndi kwa Kachisi, Maziko ako adzaikidwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help