NYIMBO YA SOLOMONI 7 - Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mas. 45.13 Ha, mapazi ako akongola m'zikwakwata,

mwana wamkaziwe wa mfumu!

Pozinga m'chuuno mwako pakunga zonyezimira,

ntchito ya manja a mmisiri waluso.

2Pamchombo pako pakunga chikho choulungika,

chosasowamo vinyo wosanganika:

Pamimba pako pakunga mulu wa tirigu

wozingidwa ndi akakombo.

3Mawere ako akunga ana awiri a nswala

anabadwa limodzi.

4Khosi lako likunga nsanja yaminyanga;

maso ako akunga matawale a ku Hesiboni,

a pa chipata cha Batirabimu;

mphuno yako ikunga nsanja ya ku Lebanoni

imene iloza ku Damasiko.

5Mutu wako ukunga Karimele,

ndi tsitsi la pamtu pako likunga nsalu yofiirira;

mfumu yamangidwa ndi nkhata zake ngati wam'nsinga.

6Ha, ndiwe wokongola ndi wofunika,

bwenziwe, m'zokondweretsa!

7Msinkhu wakowu ukunga mgwalangwa,

mawere ako akunga matsango amphesa.

8Ndinati, Ndikakwera pa mgwalangwapo,

ndikagwira nthambi zake:

Mawere ako ange ngati matsango amphesa,

ndi kununkhira kwa mpweya wako ngati maula.

9M'kamwa mwako munge ngati vinyo woposa,

womeza tseketseke bwenzi langa,

wolankhulitsa milomo ya ogona tulo.

10 Mas. 45.11; Nyi. 6.3 Ndine wa wokondedwa wanga mnyamatayo,

ndine amene andifunayo.

11Tiye, bwenzi langa, tinke kuminda;

titsotse m'milaga.

12Tilawire kunka kuminda yamipesa;

tiyang'ane ngati mpesa waphuka, kunje ndi kuonetsa zipatso,

makangaza ndi kutuwa maluwa ake;

pompo ndidzakupatsa chikondi changa.

13 Gen. 30.14 Mankhwala a chikondi anunkhira,

ndi pamakomo pathu zipatso zabwino,

za mitundumitundu, zakale ndi zatsopano,

zimene ndakukundikira iwe, wokondedwa wanga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help