1 Ower. 3.10 Pamenepo mzimu wa Mulungu unagwera Azariya mwana wa Odedi,
2Yes. 55.6; Mat. 7.7; Yak. 4.8ndipo anatuluka kukomana naye Asa, nanena naye, Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.
3Hos. 3.4Masiku ambiri tsono Israele anakhala wopanda Mulungu woonayo, ndi wopanda wansembe wakuphunzitsa, ndi wopanda chilamulo;
4Deut. 4.29koma pamene anatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israele m'kusautsidwa kwao, ndi kumfuna, anampeza.
5Ndipo nthawi zija panalibe mtendere kwa iye wakutuluka, kapena kwa iye wakulowa, koma mavuto aakulu anagwera onse okhala m'maikomo.
6Mat. 24.7Ndipo anapasulidwa, mtundu wa anthu kupasula unzake, ndi mudzi kupasula mudzi; pakuti Mulungu anawavuta ndi masautso ali onse.
7Yos. 1.6-7, 9Koma limbikani inu, manja anu asalende; pakuti ku ntchito yanu kuli mphotho.
8Ndipo pakumva Asa mau awa, ndi chinenero cha Odedi mneneriyo, analimbika mtima, nachotsa zonyansazo m'dziko lonse la Yuda ndi Benjamini, ndi m'midzi adailanda ku mapiri a Efuremu; nakonza guwa la nsembe la Yehova lokhala pakhomo pachipinda cholowera cha nyumba ya Yehova.
92Mbi. 11.16Namemeza onse a m'Yuda ndi m'Benjamini, ndi iwo akukhala nao ochokera ku Efuremu, ndi Manase, ndi Simeoni; pakuti anamdzera ochuluka ochokera ku Israele, pamene anaona kuti Yehova Mulungu wake anali naye.
10Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu mwezi wachitatu, Asa atakhala mfumu zaka khumi ndi zinai.
112Mbi. 14.13Naphera Yehova nsembe tsiku lija za zofunkha adabwera nazo, ng'ombe mazana asanu ndi awiri, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri.
12Neh. 10.29Nalowa chipangano chakufuna Yehova Mulungu wa makolo ao ndi mtima wao wonse, ndi moyo wao wonse;
13ndi kuti yense wosafuna Yehova Mulungu wa Israele aphedwe, ngakhale wamng'ono kapena wamkulu, wamwamuna kapena wamkazi.
14Ndipo analumbira kwa Yehova ndi mau akulu, ndi kufuula ndi mphalasa ndi malipenga.
15Ndipo Yuda yense anakondwera nalo lumbirolo; pakuti adalumbira ndi mtima wao wonse, namfunafuna ndi chifuno chao chonse; ndipo anampeza; ndi Yehova anawapumulitsa pozungulirapo.
161Maf. 15.13-15Maaka yemwe, mai wake wa Asa, mfumu, namchotsa uyu asakhalenso mai wa ufumu, popeza anapanga fanizo lolaula; ndipo Asa analikha fanizolo, naliphwanyaphwanya, nalitenthera ku mtsinje wa Kidroni.
17Chinkana misanje siinachotsedwa m'Israele, mtima wa Asa unali wangwiro masiku ake onse.
18Ndipo analowa nazo zopatulika za atate wake, ndi zopatulika zakezake, kunyumba ya Mulungu; ndizo siliva, ndi golide, ndi zipangizo.
19Ndipo panalibenso nkhondo mpaka Asa atakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zinai.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.