YUDA Mau Oyamba - Buku Lopatulika Bible 2014
Mau Oyamba Kalata yolembedwa ndi mtumwi Yuda analembedwa pofuna kuwachenjeza za aphunzitsi onyenga amene amadzitcha okhulupirira. Mkalata iyi yachidule imene nkhani zake zikufanana ndi za mu Kalata yachiwiri yolembedwa ndi mtumwi Petro, ndipo wolembayo akuwalimbikitsa awerengi ake kuti “mulimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima”.Za mkatimuMau oyamba 1.1-2Khalidwe labwino, chiphunzitso, ndi mathero a aphunzitsi onyenga 1.3-16Awalimbikitsa asunge chikhulupiriro 1.17-23Mdalitso 1.24-25