MASALIMO 40 - Buku Lopatulika Bible 2014

Alemekeza chipulumutso cha Mulungu, alalikira poyera chilungamo cha MulunguKwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Mas. 27.14 Kuyembekeza ndayembekeza Yehova;

ndipo anandilola, namva kufuula kwanga.

2 Mas. 27.5 Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko,

ndi m'thope la pachithaphwi;

nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.

3 Mas. 33.3 Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga,

chilemekezo cha kwa Mulungu wanga;

ambiri adzachiona, nadzaopa,

ndipo adzakhulupirira Yehova.

4 Mas. 34.8 Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika;

wosasamala odzikuza, ndi opatukira kubodza.

5 Eks. 15.11 Inu, Yehova, Mulungu wanga,

zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri,

ndipo zolingirira zanu za pa ife;

palibe wina wozifotokozera Inu;

ndikazisimba ndi kuzitchula,

zindichulukira kuziwerenga.

6 1Sam. 15.22; Mas. 51.16; Yes. 1.11; Mat. 9.13 Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo;

mwanditsegula makutu.

Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapempha.

7Pamenepo ndinati, Taonani, ndadza;

m'buku mwalembedwa za Ine,

8 Yoh. 4.34; Aro. 7.22 kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga;

ndipo malamulo anu ali m'kati mwamtima mwanga.

9 Mas. 22.22, 25 Ndalalikira chilungamo mu msonkhano waukulu;

onani, sindidzaletsa milomo yanga,

mudziwa ndinu Yehova.

10 Mac. 20.27 Chilungamo chanu sindinachibisa m'kati mwamtima mwanga;

chikhulupiriko chanu ndi chipulumutso chanu ndinachinena;

chifundo chanu ndi choonadi chanu

sindinachibisira msonkhano waukulu.

11 Mas. 61.7 Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu,

chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.

12 Mas. 38.4 Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga,

zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya;

ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.

13 Mas. 70.1-5 Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni;

fulumirani kudzandithandiza, Yehova.

14Achite manyazi nadodome

iwo akulondola moyo wanga kuti auononge.

Abwerere m'mbuyo, nachite manyazi

iwo okondwera kundichitira choipa.

15Apululuke, mobwezera manyazi ao

amene anena nane, Hede, hede.

16 Mas. 35.27 Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu;

iwo akukonda chipulumutso chanu

asaleke kunena, Abuke Yehova.

17 1Pet. 5.7 Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi;

koma Ambuye andikumbukira ine.

Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga,

musamachedwa, Mulungu wanga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help