1Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,
2Nenani nao ana a Israele, nimuti nao, Pamene mwamuna aliyense ali ndi nthenda yakukha m'thupi mwake, akhale wodetsedwa, chifukwa cha kukha kwake.
3Ndipo kudetsedwa kwa kukha kwake ndiko: ngakhale chakukhacho chituluka m'thupi mwake, ngakhale chaleka m'thupi mwake, ndiko kumdetsa kwake.
4Kama aliyense agonapo wakukhayo ali wodetsedwa; ndi chinthu chilichonse achikhalira chili chodetsedwa.
5Ndipo munthu aliyense wakukhudza kama wake azitsuka zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
6Ndipo iye wakukhalira chinthu chilichonse adachikhalira wakukhayo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
7Ndipo iye wakukhudza thupi la uyo wakukhayo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
8Ndipo wakukhayo akalavulira wina woyera; pamenepo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
9Ndipo mbereko iliyonse akwerapo wakukhayo ili yodetsedwa.
10Ndipo munthu aliyense akakhudza kanthu kalikonse kadali pansi pake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo iye wakunyamula zimenezo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
11Ndipo munthu aliyense wakukhayo akamkhudza, osasambatu m'manja m'madzi, atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
12Ndipo zotengera zadothi wazikhudza wakukhayo, aziphwanye; ndi zamtengo, azitsuke ndi madzi.
13Ndipo wakukhayo atayeretsedwa ku kukha kwake, adziwerengere masiku asanu ndi awiri akhale a kuyeretsa kwake, natsuke zovala zake; nasambe thupi lake ndi madzi oyenda, nadzakhala woyera.
14Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike pamaso pa Yehova pa khomo la chihema chokomanako, nazipereke kwa wansembe;
15ndipo wansembe azipereke izo, imodzi ikhale nsembe yauchimo, ndi ina nsembe yopsereza; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova chifukwa cha kukha kwake.
16Ndipo munthu aliyense akagona uipa, azisamba thupi lake lonse ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufukira madzulo.
17Ndipo chovala chilichonse, ndi chikopa chilichonse, anagona uipa pamenepo azitsuke ndi madzi, nizidzakhala zodetsedwa kufikira madzulo.
18Mkazi yemwe, mwamuna atagona naye, onse awiri asambe ndi madzi, nadzakhala odetsedwa kufikira madzulo.
19Ndipo ngati mkazi ali ndi nthenda yakukha, ndi kukha kwake nkwa mwazi m'thupi mwake, akhale padera masiku asanu ndi awiri; ndipo aliyense amkhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
20Ndipo chinthu chilichonse agonapo pokhala ali padera nchodetsedwa; ndi chinthu chilichonse akhalapo nchodetsa.
21Ndipo aliyense akhudza kama wake azitsuka zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
22Ndipo aliyense akhudza chinthu chilichonse akhalapo iye, atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
23Ndipo chikakhala pakama, kapena pa chinthu chilichonse akhalapo iye, atachikhudza, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
24Ndipo ngati mwamuna aliyense agona naye, ndi kudetsa kwake kukhala pa iye, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; ndipo kama aliyense agonapo ali wodetsedwa.
25 Mat. 9.20 Ndipo mkazi akakhala ndi kukha mwazi masiku ambiri, osati masiku a kuoloka kwake, kapena akamakha kupitirira nthawi ya kuoloka kwake; masiku onse chilinkukha chomdetsa chake, adzakhala wodetsedwa, monga masiku a kuoloka kwake.
26Kama aliyense agonapo masiku a kukha kwake akhale ngati kama wa kuoloka kwake; ndi chinthu chilichonse akhalapo chili chodetsedwa, ngati kudetsa kwa kuoloka kwake.
27Ndipo munthu aliyense akakhudza zimenezi adzakhala wodetsedwa, natsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
28Koma akayeretsedwa kukha kwake, adziwerengere masiku asanu ndi awiri, ndipo atatero adzakhala woyeretsedwa.
29Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike nazo kwa wansembe ku khomo la chihema chokomanako.
30Ndipo wansembe apereke limodzi likhale nsembe yauchimo, ndi linalo likhale nsembe yopsereza; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova chifukwa cha kukha kwake komdetsa.
31Motero muzipatula ana a Israele kwa kudetsedwa kwao; angafe m'kudetsedwa kwao, pamene adetsa Kachisi wanga ali pakati pao.
32Ichi ndi chilamulo cha wakukha, ndi cha iye wakugona uipa, kuti kumkhalitse wodetsedwa;
33ndi cha mkazi alinkudwala ndi kudetsedwa kwake, ndi cha iye alikukha kapena mwamuna, kapena mkazi, ndi cha iye agona ndi mkazi wodetsedwa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.