MASALIMO 41 - Buku Lopatulika Bible 2014

Mulungu adalitsa wosamalira osauka. Adani ndi mabwenzi amchitira Davide zoipa, Mulungu amlanditseKwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Miy. 14.21 Wodala iye amene asamalira wosauka!

Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa.

2 Miy. 14.21 Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo,

ndipo adzadalitsika pa dziko lapansi,

ndipo musampereke ku chifuniro cha adani ake.

3 Miy. 14.21 Yehova adzamgwiriziza pa kama wodwalira;

podwala iye mukonza pogona pake.

4 Mas. 147.3 Ndinati ine, Mundichitire chifundo, Yehova;

Chiritsani mtima wanga; pakuti ndachimwira Inu.

5Adani anga andinenera choipa, ndi kuti,

adzafa liti, ndi kutayika dzina lake?

6 Miy. 26.24-26 Ndipo akadza kundiona wina angonena bodza;

mumtima mwake adzisonkhera zopanda pake,

akanka nayenda namakanena.

7Onse akudana nane andinong'onezerana;

apangana chondiipsa ine.

8Chamgwera chinthu choopsa, ati;

popeza ali gonire sadzaukanso.

9 2Sam. 15.12; Yoh. 13.18 Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira,

ndiye amene adadyako mkate wanga,

anandikwezera chidendene chake.

10Koma Inu, Yehova, mundichitire chifundo, ndipo mundiutse,

kuti ndiwabwezere.

11Umo ndidziwa kuti mukondwera ndi ine,

popeza mdani wanga sandiseka.

12 Yob. 36.7 Ndipo ine, mundigwirizize m'ungwiro wanga,

ndipo mundiike pankhope panu kunthawi yamuyaya.

13Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele,

kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha.

Amen, ndi Amen.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help